UDF siidaganize za mgwirizano—Atupele
Phungu wa chipani cha United Democratic Front (UDF) wakummwera kwa boma la Balaka, Lucius Banda, wapempha chipanicho kuti chilowe mu mgwirizano ndi gulu la United Transformation Movement (UTM) kuti chidzachite bwino pa zisankho zapatatu za chaka cha mawa.
Koma mtsogoleri wa chipanicho, Atupele Muluzi, adauza msonkhano waukulu wa UDF womwe udachitikira mu mzinda wa Blantyre kuti atsogoleri omwe msonkhanowo wasankha akambirana momwe chipanicho chiyendere mpaka kukafika ku zisankhozo.
Msonkhanowo usadachitike mlembi wamkulu wa chipanicho, Kandi Padambo, adati akuluakulu achipanicho aunika ngati kuli koyenera kulowa mu mgwirizano kapena ayi.
“Tsogolo labwino la UDF ndi mgwirizano ndi gulu la UTM chifukwa ku Democratic Progressive Party komwe aphungu athu ambiri akhala kwa zaka zitatu palibe chomwe apindulako.
“Kunena mosapsyatira, DPP ikugwiritsa ntchito UDF kuti ilowe m’madera mwake ndipo ndili ndi zitsanzo,” adatero Banda.
Mmbuyomu Lucius adalengeza kuti adzapikitsana ndi Muluzi pa msonkhanowo, koma pomwe umayamba adasintha maganizo moti sadapitekonso.
Msonkhano waukulu wa UDF wasankhanso Muluzi kukhala mtsogoleri wa chipanicho ndipo womutsatira m’chigawo cha kummawa ndi Lillian Patel, kumpoto ndi Victoria Mponela pamene wa kummwera ndi Lancy Mbewe.
Padambo watenganso udindo wa mlembi wamkulu, Carlton Sichinga ndi msungichuma, Abubaker Mbaya ndi mkulu wa zokonzakonza ndipo wachiwiri wake ndi Andrew Mkana pamene Ken Ndanga ndi wofalitsa nkhani.
Mkulu wa UTM ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Saulos Chilima, yemwe adatuluka chipani cha DPP mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, atakana kutula pansi udindo kuti Chilima adzaimire chipanicho pa zisankho za chaka cha mawa.