Nkhani

MCP siidakhutire ndi kalembera

Listen to this article

Chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chati ngakhale ndime yachiwiri ya kalembera wa zisankho yayenda bwino poyerekeza ndi yoyamba, MEC iganizire zobwereranso m’maboma omwe yadutsamo kale kaamba koti anthu ambiri sadalembetse.

Koma mkulu wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC), Jane Ansah, wati ndi wokhutira ndi mmene kalembera wayendera m’gawo lachiwiri.

Ansah: Zinthu zayenda bwino

Kalembera wa m’gawoli amachitikira m’maboma a Dowa, Ntchisi, Mchinji ndi Nkhotakota.

Malingana ndi lipoti lomwe MEC yatulutsa, mwa anthu 1 048 080 omwe limayembekezera kulembetsa, anthu 875 138 ndiwo alembetsa.

Chiwerengerochi chikutanthauza kuti mwa anthu 100 aliwonse omwe amayenera kulembetsa, 83 ndiwo alembetsa zomwe zachititsa mlembi wa MCP, Maurice Munthali, kupempha MEC kuti ibwererenso m’mabomawo.

“Pali chosekerera apa? Tiyenera kuyandikira kwenikweni ku chiwerengero cha anthu omwe tidayenera kuwalembetsa, koma zomwe zachitika apa zikusonyeza poyera kuti anthu ambiri sadalembetse. Choncho MEC iyenera kubwereranso m’mabomawo,” adatero Munthali.

Mlembiyu adati mu ufulu wa demokalase ngakhale kusiya munthu mmodzi zimakhala zodandaulitsa.

Mkulu wa bungwe la Human Rights Defenders, Timothy Mtambo, akugwirizana ndi MCP kuti kalemberayo adzachitikenso kaamba koti munthu aliyense ali ndi ufulu wovota.

Mkulu wa bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) Trust, Ollen

Mwalubunju, adati zinthu m’gawo lachiwiri zasintha kwambiri poyerekeza ndi loyamba.

“Pali kusintha kwakukulu chifukwa m’gawo loyamba timanena za anthu 73 pa anthu 100 aliwonse, koma pano tikunena za anthu 83 pa anthu 100 aliwonse. Izi zikutanthauza kuti zinthu zikusintha,” adatero Mwalubunju.

Pazaganizo lobwereranso m’maboma momwe kalemberayu wachitika kale, Mwalubunju adati mpofunika kudikira kaye kuti MEC iwone mmene zinthu zitayendere m’maboma ena.

Malingana ndi kalata ya MEC yomwe yasayinidwa ndi woyang’anira zisankho, Sam Alfandika, mwa anthu onse omwe alembetsa m’gawo lachiwiriri, 462 925 ndi amayi ndipo 411 706 ndi abambo.

Ansah adati zinthu zasintha kwambiri m’gawoli poyerekeza ndi mmene zidaliri m’gawo loyamba m’maboma a Kasungu, Dedza ndi Salima.

“Mavuto a akulu omwe takumana nawo ndi kuwonongeka kwa zipangizo zogwirira ntchito, kusowa kwa dizilo wa ma generator athu, komanso zipangizo zoyendera mphamvu ya dzuwa sizimagwira bwino ntchito moyenera potengera ndi mmene nyengo ilili.

“Mavutowa tawapezera njira zake moti kukubwera konseku, anthu

ayembekezere kalembera wabwino,” iye adatero.

Ansah adati MEC siidapange chiganizo pa nkhani yobwereranso m’maboma momwe yadutsamo kale.

Related Articles

Back to top button