Nkhani

Ufulu usasokoneze umunthu, chipembedzo

Pomwe dziko la Malawi lakwanitsa zaka 60 mu ufulu wodzilamulira, atsogoleri ena a mipingo ati zili bwino komanso pakuyenera kusamalitsa kumbali yoteteza dziko ku ziphunzitso zachilendo m’dzina la maufulu.

Mbusa Patrick Gondwe wa Mpingo wa Efatha mu mzinda wa Blantyre wati n’koyenera ndithu kuti Amalawi anyadire kaamba koti zambiri zabwino zachitika m’nyengo ya ufulu wodzilamulira, ndipo ku mbali ya chipembezo anthu sangasowe zipatso zolozeka.

Kawinga: Tizipempherera atsogoleri

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera adatsogolera mwambo wa mapemphero wokumbukira ufulu wodzilamulira umene udachitikirza ku Bingu International Convention Centre mumzinda wa Lilongwe Loweruka lapitalo.

A Gondwe adatchula kubadwa kwa mipingo yosiyanasiyana komanso kupemphera monga momwe munthu kapena mpingo ungafunire mopanda kuletsedwa ngati zina mwa zosintha zimene zadza.

“Pali ufulu ochita zinthu momasuka monga kuyambitsa mipingo, makampani, kapena mabungwe, kuphatikiza kupanga mabizinesi pophatikizira kuyendetsa dziko.

“A mipingo tili ndi mwayi wopembedza Mulungu osacheukacheuka komanso motsogozedwa ndi Amalawi anzathu. Ndipo timatha kupemphera m’chilankhulo chilichonse.”

Komabe mbusayo adaunikira kuti pomwe Amalawi akusangalarira ufulu, mtendere komanso mwayi wogwiritsa ntchito maufulu osiyanasiyana, n’koyenera kukhala osamalitsa popeza maufulu ena ndi otsutsananso ndi chikhalidwe cha dziko lino komanso chiphunzitso cha Mulungu

“Ufulu uli apo, tikuyenera kuzindikira kuti Genesisi 1 vesi ya 26 imatiuza zoti tidalengedwa m’chifaniziro ndi chikhalidwe cha Mulungu, kotero zochita zathu zikuyenera kuonetsa kuti ndife chifanizo cha Namalengayo, osati kumangotengeka ndi zikhalidwe kapena ziphunzitso zotsutsana ndi Mulungu kapenanso chikhalidwe chathu,” adalangiza motero mbusayo.

Mlembi wamkulu ku mpingo wa Matiki Assemblies of God m’boma la Nkhotakota mbusa Ted Kukada adati chisangalalo cha ufulu si kuti chatsamira ku mbali ya ndale yokha koma m’madera ambiri a umoyo ndi chikhalidwe.

“Mukhoza kuona kuti pali mgwirizano wabwino pakati pa mipingo, mabungwe a chipembedzo ndi ena otero zomwe zikuchititsa kuti kusamakhale kukokanakokana kapena kuonerana m’botolo kumbali ya zipembedzo. Ndipo n’zonyaditsa kuti Amalawi ambiri akutsogolera mipingo komanso mabungwe achipembezo,” adatero iwo.

Ndipo Bishopu Prestone Kasito a mpingo wa Hosanna International Church m’boma la Mulanje ati chitsanzo chomwe mtsogoleri woyamba wa Chimalawi, Dr Hastings Kamuzu Banda adaonetsa choti n’zotheka kukhala ndi chipambano pogwiritsa chabe mawu, dziko la Malawi lakhala likugwiritsa ntchito mawu pofuna kusintha zinthu, osati nkhondo.

Sheikh Jafaar Kawinga, adati posangalalira ufulu umenewu pakuyenera kukhalanso nthawi yomapempherera atsogoleri akale komanso omwe ali pa maudindo padakalipano.

“Tiyamikire kuti maziko omwe adakhazikitsa pulezidenti Banda akupitirirabe pano popeza tikadali mu ufulu ndi mtendere chomwe chili chinthu chonyaditsa,” adatero a Kawinga.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button