Wa zaka 19 apha mkazi wake wa zaka 16
Nkhanza za m’banja zikuchuluka m’dziko muno moti kalembera wa 2015 adawonetsa kuti mwa amayi 100 alionse omwe adakwatiwapo 42 adachitiridwako nkhanza za mitundu yosiyanasiyana.
Chiwerengerochi chikuposa cha dziko lonse chomwe chili pa 35 mwa amayi 100 alionse omwe adalowako m’banja.
Malinga ndi kafukufukuyo, maukwati a ana n’chimodzi mwa zifukwa zomwe zimakolezera nkhanzazo chifukwa awiriwo amakhala osakhwima m’mutu kotero sangakwanitse kupilira mavuto ndi nkhawa zina zomwe zimapezeka m’banja.
Izi zikupherezera zomwe akadaulo mdziko muno akhala akumenyera nkhondo kuti anthu asamalowe m’banja asadakwane zaka 18 monganso momwe malamulo adziko lino amanenera.
M’boma la Mzimba, bambo wa zaka 19 Benson Phiri wapha mkazi wake Pansipalenga Mphepo wa zaka 16 pomumenya ndi mpini wa khasu m’mutu atasemphana nkhani za m’banja.
Mneneri wapolisi m’bomalo a Peter Botha atsimikiza kuti pa 9 November 2022 m’ma 8 Koloko madzulo banjalo lidasemphana zochita ndipo mkati mokangana Phiri adamenya Mphepo ndi mpini wa khasu m’mutu n’kukomoleratu.
“Mayiyo adakafera kuchipatala tsiku lotsatiralo (pa 10 November 2022) chifukwa chovulala kwambiri mmutu ndipo bamboyo akayankha mlandu wakupha posachedwapa,” atero a Botha.
Malingana ndi malamulo a dziko lino, banjalo silimayenera kuchitika chifukwa mkaziyo adali ndi zaka 16 pomwe malamulo omwe boma lidakhazikitsa m’chaka cha 2015 amavomereza ukwati munthu akafika zaka 18.
Kafukufuku wa BMC Public Health ndime 1 350 ikusonyeza kuti amayi 42 mwa amayi 100 alionse a zaka za pakati pa 20 ndi 24 m’dziko muno adalowa m’banja asadafike zaka 18 ndipo amayi 13 mwa amayiwo adalawapo banja pomwe amakwanitsa zaka 13 zakubadwa.
Womenyera ufulu wa ana a Memory Chisenga ati potengera malamulo, banja la Phiri ndi Mphepo lidali losavomerezeka chifukwa mkaziyo adali mwana wosayenera kulowa m’banja.
“Tiyambe taunika adindo monga makolo, amfumu ndi makomiti oona zaufulu wa ana ngati aliko kwawoko chifukwa samayenera kulola kuti banja limenero litheke,” atero a Chisenga.
Iwo ati vuto lomwe lilipo ndi loti m’dziko muno timajijirika chinthu chikachitika mmalo moti tizikonzekera kuti chinthucho chisachitike.
Iwo ati msungwana wa zaka 16 maganizo ake amakhala akadali a chibwana kotero akhoza kupanga zosagwirizana ndi m’banja osadziwa kuti akulakwitsa ndipo mapeto ake zomwe angamakumane nazo m’banjamo ndi nkhanza.
Woyang’anira za ana kuunduna owona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi amuna a MacNight Kalanda ati banja la ku Mzimbalo udali kale mulandu ngakhale adali asadachitane nkhanzayo.
Iwo ati unduna wawo ukuunika ndondomeko zotetezera ana zomwe zakhala zikugwira ntchito kuti aone zomwe zikugwira ndi zomwe sizikugwira kuti asinthe machitidwe.
“Takhala tikulimbana ndi mchitidwewu koma pakuoneka kuti pali zobwezera mmbuyo zina zomwe tikufuna kufufuza. Koma ntchitoyo ikuyenda chifukwa tachepetsa chiwerengero cha amayi okwatiwa ali ana kuchoka pa 42 kufika pa 37 pa 100 alionse,” atero a Kalanda.
Malemu Mphepo amachokera m’mudzi mwa Zawanje Mphepo kwa T/A Chindi m’boma la Mzimba.