Woganiziridwa kuzembetsa anthu wagwidwa
Mwambi woti khoswe wa pa tsindwi adaulula wa pa dzala wapherezera ku Mulanje komwe mlandu wa pa msewu wavumbulutsa mulandu wozembetsa anthu.
Malingana ndi mneneri was apolisi m’boma la Mulanje a Innocent Moses, kugwidwa kwa dilaiva yemwe minibasi yake yopangira malonda pa msewu inapezeka mbali yomwe minibasiyo inalibe chilolezo kunaika pa mbalambanda yemwe anapanga hayala minibasiyo.
“N’zoona ndithu kuti a Nyson Gomba a zaka 26 anamangidwa pa nkhani yozembetsa anthu ndipo nkhani yawo ili ku khoti. Koma izi zinachitika pambuyo poti apolisi a pansewu anagwira minibasi yomwe inapezeka ku Mulanje pomwe inalibe ndondomeko zoyenerera malinga ndi zomwe zimaperekedwa ku ma minibasi opanga bizinesi pa msewu. Malinga ndi kulakwitsako, dalaivala amayenera kulipira chindapusa.
“Apa ndi pomwe Dalaivala anauza a polisi kuti yemwe anapanga hayala minibasiyo kuchokera ku Blantyre anali asanamupatse ndalama ina yokwanira K160 000. Ndipo muukadaulo wawo, apolisi anakwanitsa kufunsa opanga hayalayo ndipo mpomwe zinadziwika kuti anthu omwe anali mu minibasiyo amapita nawo mdziko la Mozambique komwe amayembekezera kukagwira ntchito zosiyanasiyana,” Moses anatero
Koma atatengeredwa ku bwalo la milandu la Senior Resident Magistrate, oganizilidwayu anaukana mulandu womwe anapatsidwa wozembetsa anthu, zomwe zinapangitsa kuti oimira mulandu mbali ya Boma abweretsa mboni zingapo.
Senior resident magistrate Gloria Mwatiwamba atamva mbali zonse anaona kuti nkoyenera kuimitsa milanduyo kuti adzapereke chigamulo lolemba likubwerali pa July 22 2024. Ndipo poyembekezera tsikuli, Gomba yemwe amachokera mmudzi wa Matipwiri mdera la mfumu yaikulu Mabuka m’boma la Mulanje, akusungidwa ku Mulanje Prison.