Nkhani

Za anamapopa sizikuzilala

Listen to this article

Nkhani ya anamapopa ikulephera kutha. Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika atangomaliza kuyendera maboma amene anthu angapo aphedwa powaganizira kuti ndi wopopa magazi.

Sabata yomweyi, munthu wina wa zaka 22 adaphedwa ku Chileka mumzinda wa Blantyre pomuganizira kuti ndiwopopa magazi. Anthu okwiya adaswa polisi ya pa Chatha kuderalo atamupeza atagona m’munda wina, chonsecho mkuluyo anali wakhunyu ndipo amachokera kuchipatala.

Mbale wa mfumu Mtenje, Henry Kawisa (Kumanja) kuyendera khola

Ndipo mkulu winanso adaphedwa ku Balaka atapezeka akuyendayenda mbandakucha. Ndipo kwa Mtenje ku Chigumula mumzinda wa Blantyre, anthu adathyola khola la mfumu ya deralo ndi kubamo nkhumba 12, kuswa mawindo a nyumba yake mpaka kupulumutsidwa ndi apolisi.

Ndipo ena adachita zionetsero ngakhale pakati pausiku ku Bangwe, kwa Kachere, Machinjiri ndi Sigelege.

Zonsezitu zimachitika pomwe kuyambira Lachisanu mpaka Lolemba Mutharika adayendera maboma a Mulanje, Nsanje, Phalombe ndi Chiradzulu kumva anthu opulumuka ku ‘opopa magazi’, amene amaganiziridwa kuti ndi anamapopa komanso mafumu.

Chachikulu chimene chidatuluka pamisonkhanoyo n’choti mfumu yaikulu ya Alhomwe Paramount Ngolongoliwa idati akuchita izi ndi amatsenga ochokera ku Mozambique. Mfumuyo idapempha Mutharika kuti awasiyire zonse athane nawo m’matsenga.

“Mundipatse masiku 21, ife mafumu anu tithana nawo. Sangamachoke ku Mozambique kudzatiseweretsa kuno ngati tilibe ufiti. Tithana nawo basi,” adatero Ngolongoliwa.

Pamene adapempha Amalawi kusunga bata, makamaka pomwe akuganizira ena kukhala opopa magazi, Mutharika adati ngati nkhanizi ndi za matsenga azisiya m’manja mwa Ngolongoliwa ndi mafumu ena.

Koma mlembi wamkulu wa bungwe la oimira ena pamilandu la Malawi Law Society (MLS) Michael Goba wati ngati Ngolongoliwa adanena izi adaphwanya gawo 6 la malamulo okhudza nkhani za ufiti ndipo akhonza kumangidwa ndi kufunsidwa mafunso pakhoti.

“Gawoli limati onena kapena zochita zake zikusonyeka kuti ndi mthakati kapena wochita zaufiti adzalipa $50 (K36 500) ndi kukhala kundende zaka 10. Zomwe akuti zidanenedwa ndi mfumuyo ndi mlandu. Malamulo ndi wothekera kuthana ndi vutoli pokhapokha adindo a mphamvu zotero atawagwiritsa bwino ntchito,” adatero Chipeta.

Iye adati n’zokhumudwitsa ngati Ngolongoliwa adanenadi izi chifukwa udindo wake ndi wolemekezeka komanso uli pansi pa malamulo a dziko lino.

Pankhani yokhudza ufiti m’dziko muno, Chipeta adati polingalira mwakuya ndi povuta kunena kuti ulipo kapena ayo chifukwa ngati chipembedzo zimatengera katanthauziridwe ka mphamvu zapaderazi ndi zikhulupiriro za anthu. Iye adaonjezeranso kuti pachifukwachi sunganeneretu kuti munthu angachite kapena kusachita ufiti m’dziko lomwe silivomereza mchitidwewu.

Malingana ndi mkulu wa bungwe la Association of Secular Humanism (ASH) George Thindwa, yemwe amalimbikitsa ganizo loti ufiti kulibe, Ngolongoliwa sadathandize kuthana ndi mpheketserayi ndipo amayenera kutsata malamulo a dziko lino chifukwa anamapopawo kulibe.

Related Articles

Back to top button