Nkhani

Zaka 10 kwa bambo wofuna kugwiririra

Listen to this article

Bwalo la milandu la majisitileti ku Kasungu Lachitatu lidagamula bambo wa zaka 26, a Geoffrey Kwenda kuti akaseweze kundende zaka 10 pofuna kugwirira msungwana wa zaka 17.

Malinga ndi wapolisi woimira boma pamilandu a Ulemu Bota, adauza bwalolo kuti pa 5 September 2021 cha m’ma 9 m’mawa, msungwanayo adapita kumtsinje kukachapa komanso ziwiya za kukhitchini.

Koma ali uko, woganiziridwayo adafika n’kupempha kapu yoti amwere madzi koma akupereka kapuyo, mkuluyo adayamba kumutchetcherera.

“Ataona kuti bamboyo akufuna kumuchita chipongwe, adayamba kuthawa koma njondayo idamuthamangitsa mpaka kumugwira n’kuyamba kuyesera kuchita naye zadama koma iye adakuwa ndiye anthu adabwera kudzamulanditsa,” adatero a Bota.

Malinga ndi mneneri wa apolisi ku Kasungu a Joseph Kachikho, anthu a m’mudzimo adagwira a Kwenda ndi kukampereka kupolisi.

M’bwalo la milandulo, iwo adaukana mlandu wofuna kugwiririra, zomwe zidachititsa kuti apolisi abweretse mboni zitatu kuti atsimikize mlanduwo.

A Bota adati wozengedwa mlanduyo apatsidwe chilango chokakhala kundende chifukwa milandu yotere ikuchulukira m’bomalo komanso dziko lonse lino.

“Ndipo khalidweli limadzetsa kuzunzika m’maganizo kwa amene achitiridwa nkhanza,” adatero iwo.

Koma podandaula, a Kwenda adapempha bwalolo kuti liwakhululukire chifukwa ali ndi udindo waukulu pabanja lawo komanso akusamalira ambuye awo omwe ndi wokolamba.

Koma majisitileti Jones Masula adapereka zaka 10 kwa mkuluyo kuti ena angakhale ndi malingaliro otere asachitenso chimodzimodzi. A Kwenda amahokera m’mudzi mwa Nyemba kwa T/A Chidzuma m’bomalo.

Related Articles

Back to top button