Zaka 59 pa ufulu tapindulanji
Kadaulo pa ndale a George Phiri ati palibe chifukwa chomveka choti dziko la Malawi lizikondwerera ufulu wodziimirira palokha chifukwa m’zambiri limadalira maiko ndi mabungwe ena.
Lachinayi lapitali dziko la Malawi limakondwerera kuti lakwanitsa zaka 59 wodziimira pa lokha ndipo bajeti ya chikondwererocho idali K320 miliyoni.
Chikonwererocho chidayamba ndi mwambo wa mapemphero ku Bingu International Convention Centre (BICC) mumzinda wa Lilongwe ndipo chikondwerero chachikulu chidachitika kubwalo la Bingu National Stadium kumene mlendo wolemekezeka kwambiri adali mtsogoleri wa dziko la Tanzania, mai Samia Suluhu Hassan.
Koma a Phiri ati zikutanthauzanji kusakaza ndalama zochuluka choncho kupanga chikondwerero chomwe tanthauzo lake silioneka poti zambiri timapanga ndi thandizo la mabungwe ndi mayiko ena.
“Zoona tingaononge K320 miliyoni kukondwerera ufulu wodzilamulira chonsecho mtsogoleli wathu akulowera uku ndi uko kukapempha thandizo?
“Tikuyendetsa dziko ndi thandizo koma n’kumati ndife odziyimilira patokha zoona? Tikuchita kusowa ndalama zakunja koma n’kumati tili paufulu wodzilamulira. Tisinthe kaye othandiza azibwera tokha tili mpogwira,” atero a Phiri.
Ndipo polankhula pa mwambo wa Lachinayi, a Chakwera adati chifukwa cha ufulu wodziimirira, dziko la Malawi ladutsa m’zambiri koma lidapilira zonsezo ndipo likuyesetsa palokha kuchilimika kuti litukuke.
“Ngakhale takumana ndi mikwingwirima y o s i y a n a s i y a n a , sizidatibwezele mmbuyo pamasomphenya athu a Malawi 2063 ofuna kuti dziko lathu likwele kuchoka pomwe lili,” adatero a Chakwera.
Iwo adati zitukuko zosiyanasiyana zomwe zikuchitika m’madera osiyanasiyananso ndi umboni wot i kupita kwa zaka tili paufulu kukus intha z inthu koma adadandaula kuti anthu ena adyera ndiwo amabwe z e r a dz i ko mmbuyo pakuba ndalama za boma.
A Suluhu omwe adali mlendo wolemekezeka p a m w a m b o w o adayamikira dziko la Malawi chifukwa chosunga bata ndi mtendere pa zaka zonse 59 zomwe lakhala paufuluwo.
Iwo adakhuza Amalawi omwe adataya miyoyo kaamba ka namondwe wa Freddy kupitiriza pa thandizo lomwe dziko lawo lidapeleka namondweyo atangochitika kumene.
Koma pothirirapo ndemanga, Amalawi ena adati chikondwerero cha tsikuli chimangochitika mwa chizolowezi chabe chifukwa kudziimira p a t o k h a k o m w e timakondwerera sikuoneka mmalo mwake mavuto amangosinthana m’dziko muno.
A Precious Sinyangwe a mumzinda wa Lilongwe ati iwo atengapo gawo pa z ikondwe r e r o z a m t u n d u w u k o m a palibe kusintha komwe angaloze kuti Amalawi akudziyimiliradi pawokha.
“Tikunena za zaka 59 koma zambiri timadalira zakunja. Zoona ndi zakumunda zomwe monga nthochi, mazira ndizipatso zina ndi zina tizichita kuyitanitsa kuchoka kunja ngati kuti tilibe nthaka ndi madzi? Koma nkumati ndife odziyimilira patokha,” adatero a Sinyangwe.
A Mirriam Chawona nawo adati tsiku l i limangokomela kuti anthu amakhala ndi mpata wopuma koma tanthauzo l a ke limasemphana ndi momwe zinthu zikuyendela.
“Ine ndinenako pa za ngongole zomwe tili nazo. Kuchuluka kwa ngongolezo kukusonyezelatu kuti siife oyima patokha ayi timadalirabe ena. Ana omwe akubwera mtsogolo adzatifunsa mafunso woti tidzalephera kuyankha pazatanthauzo la tsikuli,” adatero a Chawona.
D z i ko l a Malawi l i d a l a n d i r a u f u l u wodzilamuli m’chaka cha 1964 ndipo kuchokera apo lidali pansi paulamiliro wa chipani chimodzi cha Malawi Congress Party (MCP) mpaka m’chaka cha 1993 pomwe kudachitika l i f e l e n d a m u a n t h u n’kusankha ulamuliro wa zipani zambiri.
Pansi paulamiliro wa zipani zambiri, dziko la Malawi lalamuliridwako ndi ma Pul e z identi osiyanasiyana asanu ndipo chaka chilichonse pa 6 July dzikoli limakumbukira ufulu wodziyilira palokha.