Nkhani

Zokhoma mu AIP

Listen to this article

Kugula zipangizo zaulimi zotsika mtengo kuli mkati koma pofika Lachiwiri pa 7 December 2021, alimi 1 miliyoni okha, mwa alimi 3.7 miliyoni omwe ali pa mndandanda wopindula, ndiwo akwanitsako kugula matumba awiri a feteleza ndi mbewu.

Malingana ndi unduna wa zamalimidwe, izi zili chomwechi chifukwa makampani ena omwe akuyenera kugulitsa nawo zipangizozo sadatumize zipangizo m’misika yawo koma undunawo wati makampaniwo akalephera kutero iwo utumiza feteleza wakuthumba la pangozi.

Mneneri waundunawo, a Gracian Lungu, ati undunawo udagula kale feteleza wokwana matani 150 000 wa kuthumba la pangozi ndipo ukaona kuti makampaniwo sakulongosoka, utulutsa fetelezayo n’kutumiza m’misika ya boma.

“Vuto lalikulu ndi makampani ena omwe akuyenera kugulitsa zipangizo ndipo sadabwere pamsika koma makampani a boma a Admarc ndi Smallholder Farmers Fertiliser Revolving Fund of Malawi [SFFRFM] akugulitsa.

“Palinso makampani ena omwe adachita bwino chaka chatha a Paramount Holdings ndi Afriventure nawo afika kale pamsika. Pulani ndi yoti zipangizo zigulitsidwe m’sabata 8 ndiye ngati makampani enawo afooke titumiza feteleza wathu m’misika,” atero a Lungu.

Koma izo zili apo, bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) lati potengera momwe nyengo ikuthamangitsirana ndi mvula, alimi omwe agula kale zipangizo ndi ochepa kwambiri.

Pulezidenti wabungwelo a Frighton Njolomole ati boma likapanda kubweramo msanga ndi kukonza zomwe zikusokoneza pulogalamu ya AIP, chaka cha mawa kukhala njala.

“Malipoti okhumudwitsa akutipeza koma ife tilibe polisi kapena asilikali oti angapite n’kukamanga omwe akusokoneza n’chifukwa chake tikuti boma litithandize,” atero a Njolomole.

M’madera ena akuti mavenda ndiwo akugula mmalo mwa alimi chifukwa mavendawo ndiwo akukwanitsa kupereka ndalama yoonjezera kwa ogulitsa zipangizozo.

Limodzi mwa maderawo ndi ku Ntchisi komwe apolisi amanga a mfumu a Mphamba, omwe akuwaganizira kuti amagulitsa zitupa zaunzika za anthu awo kwa mavenda kuti azikagulira zipangizozo m’maina a alimiwo.

Malingana ndi wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Ntchisi a Fatsani Mwale, amfumuwo adatenga zitupa zakutha za anthu 5 m’mudzi mwawo powauza kuti akufuna kukawapangitsira zatsopano, chonsecho akukagulitsa.

“Nkhaniyo idaphulika pa 3 December 2021 pomwe mmodzi mwa eni zitupazo adapita kumsika wa feteleza n’kukapeza chitupa chake chili ndi venda ndipo atafunsa adauzidwa kuti amfumu ndiwo amagulitsa zitupazo,” adatero a Mwale.

Bungwe lolimbana ndi ziphuphu la Anti-Corruption Bureau (ACB) nalo lati likufufuza nkhani za katangale zokhudza msika wa zipangizo zaulimi zotsika mtengo litalandira malipoti komanso litakadzionera lokha zina mwa zomwe zikuchitikazo.

“Tidayendera malo 100 ogulitsira zipangizo za AIP titalandira malipoti ndipo zina mwa zomwe zidatipezazo tidakazionadi zikuchitika moti tili ndi mafayilo ambiri omwe tatsegula kuti tifufuze,” adatero mkulu wa ACB a Martha Chizuma.

Alimi akuyenera kuombola thumba limodzi la feteleza pamtengo wa K7 500, kutanthauza kuti alimiwo akusowa K15 000 kuti aombole matumba awiri, koma malingana ndi zomwe ACB yapeza, alimi akukakamizidwa kuonjezera ndalama za pakati pa K3 000 ndi K10 000.

A Lungu avomereza kuti malipoti a mitundu yonseyi akufika kuunduna wawo koma ati undunawo ukumema alimiwo kuti azigwiritsa ntchito makomiti a m’madera mwawo pogwira anthu achinyengowo n’kukawapereka m’manja oyenera.

Makampani a Admarc ndi SFFRFM, omwe undunawo ukudalira kwambiri, agulitsako matani 27 190.7 a feteleza mmalo mwa 127 000 omwe akuyenera kugulitsa chaka chino.

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera adatsegulira pulogalamu ya AIP ya 2021 yomwe bajeti yake ndi K140.2 biliyoni pa 16 October 2021 ndipo K124.74 biliyoni ndi ya feteleza, K1.26 biliyoni ndi ya ziweto komanso K12.25 biliyoni ndi ya mbewu.

Related Articles

Back to top button