2019: Chaka cha mbiri pa zisankho

Chaka cha 2019 chidzalowa m’mbiri ya dziko la Malawi ngati chaka chomwe atsogoleri azipani adakwekwetsana koopsa komanso koyamba mukhoti pankhani yokhudza zotsatira za chisankho cha pulezidenti.

Pa 21 May 2019 Amalawi adalawirira kukandanda pa mzere kuti akasankhe atsogoleri awo monga ma Khansala, Aphungu ndi Pulezidenti koma nyanga zidakola pa zotsatira za mpando wa Pulezidenti.

Sadatule pansi udindo: Ansah

Pa 27 May 2019, bungwe la MEC lidalengeza kuti Peter Mutharika wa Democratic Progressive Party (DPP) adapambana pachisankho cha Pulezidenticho.

Malingana ndi bungwe la MEC, Mutharika adapeza mavoti 38.67 mwa 100 alionse, Lazarus Chakwera wa Malawi Congress Party (MCP) adapeza 35.41 ndipo Saulos Chilima wa UTM Party adapeza 20.24.

Zotsatirazo zidabweretsa mpungwepungwe waukulu moti Chilima ndi Chakwera adakasuma ku khothi ngati odandaula woyamba ndi wachiwiri mu mndandanda omwewo.

Atsogoleri awiriwa akuti Mutharika ndi MEC ngati woyankha mlandu woyamba ndi wachiwiri m’ndandanda omwewo adasokoneza chisankho cha Pulezidenti ndipo akufuna khoti ligamule kuti chisankhocho chichitikenso.

Chidadzutsa zonse ndi zikalata zolembapo momwe anthu avotera pomwe kudapezeka kuti zikalata zambiri zidafufutidwa ndi utoto wotchedwa Tippex komanso mamonitala ena sadasayine zikalata zina.

Mlandu utayambika, padali kukolanakolana pa mfundo za mboni koma mlandu udayamba kuwoneka mutu mboni imodzi ya Chakwera Daud Suleman ataonetsa khoti momwe anthu ena omwe samayenera kulowa m’makina a internet a MEC, ankagulugushira m’makinawo.

Umboni wina omwe udavuta udali wa mkulu wa bungwe la MEC Sam Alfandika yemwe adafunsidwa kuti alongosole bwino momwe Tippex adakapezekera mmalo owerengera mavoti, momwe adayankhira  madando onse 147 monga momwe Ansah adanenera polengeza zotsaira komanso kuti ndani adavomereza kugwiritsa ntchito zotsatira zokonzedwa ndi Tippex.

Alfandika yemwe patsiku loyamba adatuluka thukuta lochita kusamba mpaka khoti kuimitsidwa, adalephera kupereka maminitsi a zokambirana za makomishonala a MEC poyankha madando ndipo adavomera kuti Tippex adapezeka mmalo owerengera mavoti.

Mboni ya Mutharika Ben Phiri yemwe ndi nduna ya maboma aang’ono ndi chitukuko cha mmidzi adavomereza kuti chisankho chidakumana ndi zokhoma zambiri koma adati vuto lidali bungwe la MEC pogwiritsa ntchito anthu omwe sadaphunzitsidwe mokwanira.

Mlanduwo ukuyendetsedwa kukhoti lapadera lomwe likumvedwa ndi oweruza 5 omwe ndi Healey Potani, Mike Tembo, Dingiswayo Madise, Ivy Kamanga ndi Redson Kapindu.

M’mwezi wa June 2019, Khothili lidakana pempho la woimirira Mutharika ndi MEC loti mlanduwo angowusiya chifukwa wodandaula sadatsate ndondomeko zoyenera zosumira koma khothi lidati mlanduwo upitilire.

Mlanduwu ukunka kumapeto tsopano koma wakumana n’zokhoma zambiri monga ziletso ndi kuimaima makamaka pomwe a mbali yoyankha mlandu adapempha sabata ziwiri zoti akatolere umboni kwa omwe amayang’anira mmalo oponyera voti.

Panyengoyi padamveka mphekesera yoti okatolera umboniwo amaopseza kapena kukakamiza ndi kunyengerera oyang’anira mmalowo oponyera votiwo kuti azisayinira zikalata zomwe zidagwira ntchito koma zosasayina ndi kupereka umboni wabodza.

Pachifukwachi, otsatira zipani za MCP ndi UTM adayamba kuthotha anthuwo akafika m’dera lawo zomwe zidapangitsa kuti ntchitoyo ayionjezere ndi sabata ina.

Sabata yathayi, mbali zonse zokhudzidwa pa mlanduwo kuphatikizapo abwenzi a khoti Malawi Law Society (MLS) ndi Women Lawyers Association (WLA) adamaliza kupereka zindunji za mfundo zawo ndipo nkhani yatsala m’manja mwa majaji kuti agamule.

Share This Post

Powered by