Nkhani

Amalawi adalankhula kudzera m’zionetsero

M’chaka chomwe chikuthachi, Amalawi adamasula thumba la ukali wawo nkulankhula mokwenza makamaka pofuna kuwonetsa kuti adazindikira za ufulu ndi udindo wawo m’boma la demokalase.

Mfuwu wa Amalawiwa udamveka ponseponse maka kuyambira pomwe bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidalengeza zotsatira za chisankho cha Pulezidenti pa 27 May 2019.

Mmodzi mwa akidi kuvota pachisankho cha pa May 21

Chisankhocho chidakomera Peter Mutharika wa Democratic Progress Party (DPP) koma anthu ambiri adazizwa ndi zotsatira zomwe MEC idalengezazo.

Pa 4 June 2019, otsatira chipani cha Malawi Congress Party (MCP) adakwiya kwambiri ndi zotsatirazo mpaka adakatseka likulu la dziko la Malawi Capital Hill ku Lilongwe n’kuthotha onse ogwira ntchito kumeneko.

Ichi chidali chiyambi cha mchochombe wa zionetsero zomwe mgwirizano wa mabungwe owona za maufulu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) akhala akutsogolera zomwe zidatsala

pang’ono kukhodzokera mmabwero a ndege ndi zipata zolowera mdziko.

Zionetsero zomwe adapanga a MCP zidali zosonyeza kusakhutira ndi kulengeza kwa MEC kuti Mutharika ndiye adapambana chisankho cha pa 21 May 2019.

Pambuyo pa chionetserochi, HRDC idagwamo ndipo iyo idayima poti mkulu wa bungwe la MEC Jane Ansah atule pansi udindo wake chifukwa adalephera kuyendetsa chisankho kotero sangapitirire kutsogolera bungwelo.

M’mizinda ndi m’maboma monse mudali moto wokhawokha anthu kutentha mateyala ndi maofesi a boma kufuna kuti mawu awo amveke ndipo nkhawa zawo ziyankhidwe.

Koma ngakhale maufulu ambiri amaphwanyidwa panthawiyo monga katundu kuonongeka, anthu kutaya miyoyo, amayi kugwiriridwa ndi zina zotero, koma Jane Ansah adanenetsa kuti sangatule pansi udindo.

Koma katswiri pa ndale George Phiri adati mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika ndi Ansah akadapaga zinthu zothandiza dziko pogonjera zofuna za anthu zionetserozo zithe zisadakhodzokere kwina.

“Pali zambiri zomwe anthu zikuwapweteka monga nkhanza zomwe zidachitika kwa Nsundwe, anthu ambiri avulazidwa ena mpaka kuphedwa m’madera osiyanasiyana koma boma osaonetsa kulabadila kulikonse,” adatero Phiri.

Pano, ngakhale magulu osiyanasiyana adadzudzulapo kuti pafikapa mposafunika kupanga chilichonse chomwe chingakwenze mitima ya anthu pomwe akudikira chigamulo cha kukhoti, HRDC yanenetsa kuti siyidzabwerera mmbuyo mpaka Ansah atagonja.

Polankhula ndi Tamvani, akadaulo osiyanasiyana monga Makhumbo Muthali ndi Emilly Mkamanga komanso Boniface Chibwana wa bungwe la Chikatolika loona za chilungamo

ndi mtendere (CCJP) adati nkhani yochita zionetsero ndi ufulu wa

Amalawi ndipo nzosakhudzana ndi nkhani ya kukhoti.

Related Articles

Back to top button