2024 Amalawi adaziona
Chaka cha 2024 ndi china mwa zaka zomwe Amalawi sadzaiwala kaamba ka ziyangoyango zomwe adadutsamo mpaka ena kumalingalira za zionetsero.
Nkhani yoyamba idali ya kukwera kwa mitengo ya katundu mpakana shuga kumagula K2 800, chingwa chenichenichi mpaka kumafika K2 000 ndipo chopweteka kwambiri ndi mtengo wa fetereza yemwe amadutsa K100 000.

Alimi ambiri adalira ndi mtengowo, moti ena adapanga chiganizo chongolima popanda fetereza pomwe enanso adaiwala kamvekedwe ka tiyi poti kugula shuga n’chomwera chake kudasanduka danga la okhawo omwe amapeza ndalama.
Izi zitafikapo, Amalawi motsogozedwa ndi mabungwe adamanga zokayenda ku msewu kukatula nkhawa zawo kwa adindo kuti achitepo kanthu.
Mkulu wa bungwe la Centre for Democracy and Ecomic Development Initiative (Cdedi) a Silvester Namiwa adamema Amalawi kuti akadzilankhulire kudzera m’zionetsero.
“Boma lichitepo kanthu pa mitengo ya katundu chifukwa Amalawi akuvutika ndipo likalephera kutsitsa mitengoyo, tichita zionetsero za dziko lonse mpaka tione kusintha makamaka pa mitengo ya katundu wofunikira kwambiri pa moyo wa munthu,” adatero a Namiwa.
M’chaka chomwechi, anthu pafupifupi 7 miliyoni adakhudzidwa ndi njala yomwe akugubuduka nayo mpaka pano moti andale ena adabwera poyera n’kulengeza kuti anthu m’madera mwawo akugonera mango ndi chitedze.
Izi zimachitika nduna ya za ulimi a Sam Kawale atauza nyumba yomweyo kuti boma lakonzeka kuyamba kugawa chimanga ndi ufa kuyambira mmadera momwe njalayo yakulitsitsa koma aphungu ena adatsutsa kuti andunawo samanena zoona chifukwa boma lilibe chimanga.
“Tidapita ku nkhokwe za boma ndipo kulibe chimanga, tsono chimanga chomwe agawecho chichokera kuti? Ndi bwino kuwauza anthu zoona kusiyana n’kuwapatsa chiyembekezo cha bodza,” adatero a Sameer Sulemani pomwe ndi wa pampando wa komiti ya za ulimi.
Ululuwu uli mkati, kudagwa chilala cha mafuta a galimoto kufikira poti anthu amagona mmalo ogulitsira mafutawo kudikira pomwe agalimoto zonyamula anthu adangokwenza mitengo kuonjezera ululuwo.
Mwachitsanzo, mtunda omwe anthu amanyinyirika n’kale kukwerera K1 500 kuchoka ku Nsungwi kupita m’tauni ya Lilongwe tsopano akukwerera K2 000. Motero, mtunda wochoka ku Machinjiri mu mzinda wa Blantyre, minibasi ya K1 000 pano ili pa K1 500. Izi zikungopherezera kuti mitengo yoyendera yakwera ponseponse.
Poona izi, wa pampando wa mabungwe omenyera anthu ufulu Human Rights Defenders Coalition (HRDC) a Gift Trapence adachenjeza boma kuti likonze vuto la mafuta agalimoto zinthu zisadavute kwambiri.
“Nkhani ya mafuta si nkhani yoti tizivutika nayo chifukwa ndi zinthu zoti timayenera kukonzekera osati kumachita kudzidzimukira ayi. Apapa boma likonze vuto limeneri kapena avomereze kuti alephera,” adatero a Trapence.
Akadaulo monga mkulu wa bungwe loimira anthu ogula a John Kapito komanso komiti yoona za za chilengedwe ku Nyumba ya Malamulo a Werani Chilenga adaunikira kuti vutoli likhoza kutha ngati boma lingakwenze mtengo wa mafuta.
“Boma likamagula mafuta a galimoto kunja limagula pa mtengo wokwera pomwe kuno likugulitsa pamtengo wotsika ndiye palibe chomwe likupanga nchifukwa chake lizilephera kuyitanitsa mafuta,” adatero a Kapito.



