A Chakwera aonjezera nduna…Zachoka pa 27 kufika pa 31
Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ati asintha zina mwa nduna zawo n’kuonjezera chiwerengero cha nduna ndi achiwiri awo kufika pa 31 kuchoka pa 27 pomwe chiwerengerocho chidakhazikika mmbuyo monsemu.
Iwo adalengeza izi mu uthenga wawo wa chaka chatsopano kwa Amalawi ndipo mwa zina iwo adagawa unduna wa za maphunziro kuti ukhale m’magawo awiri wina woyang’anira za maphunziro a ukachenjede basi pomwe wina woyang’anra maphunziro a ku sekondale ndi ku pulaimale.
“Timu imeneyi indithandiza kuti tigwire ntchito molimbika ndi mwa luntha kuti nanunso miyoyo yanu m’chaka chimenechi imve kukoma, komabe monga ndimanena nthawi zonse, kuti zabwinozo zituluke, mukufunika kutengapo gawo polimbikira ntchito,” adatero a Chakwera.
Pakusinthako, a Chakwera achotsa yemwe adali nduna ya za chitetezo cha dziko a Harry Mkandawire ndi yemwe adali wachiwiri kwa nduna ya za maphunziro mayi Nancy Chaola Mdooko.
Nkhope zatsopano ndi a Ezekiel Ching’oma, mayi Jessie Kabwila omwe ndi mneneri wa chipani cha MCP, mayi Joyce Chitsulo phungu wa chipani cha DPP, a Benedicto Chambo omwenso ndi a DPP, a Peter Dimba, mayi Patricia Nangozo Kainga komanso a Noah Chimpeni a chipani cha PP.
Malingana ndi a Chakwera, a Ching’oma akukakhala nduna ya za chitetezo cha m’dziko, a Kabwila awapatsa unduna woyang’anira za maphunziro a m’sukulu za ukachenjede, ndipo a Madalitso Kambauwa Wirima atsalira ku unduna wa za maphunziro koma aziyang’anira maphunziro a pulaimale ndi sekondale.
Komwe achoka a Mkandawire ku unduna wachitetezo cha m’dziko kwapita mayi Monica Chang’anamuno omwe adali nduna ya za migodi ndipo iwo mmalo mwawo mwalowa a Ken Zikhale Ng’oma womwe mpando wawo ku chitetezo chamdziko kwapita a Ching’oma.
Yemwe adali wachiwiri kwa nduna ya za maboma ang’onoang’ono a Owen Chomanika tsopano ndi nduna ya za chilengedwe ndi kusintha kwa nyengo komwe kalelo kudali a Michael Usi asadasankhidwe kukhala wachiwiri kwa pulezidenti kulowa mmalo mwa malemu a Saulos Chilima.
A Chitsulo akukatenga malo a a Chomanika ngati wachiwiri kwa nduna ya za maboma ang’onoang’ono, a Chambo awapatsa udindo wa wachiwiri kwa nduna yazamalimidwe, a Dimba tsopano ndi achiwiri kwa nduna ya zomangamanga pomwe a Kainga ndi achiwiri kwa nduna yoona za ubale wa dziko la Malawi ndi maiko ena.
Mayi Halima Daud achoka ku unduna wa za umoyo komwe adali achiwiri n’kukakhala achiwiri kwa nduna yoona zoti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo ndi chitukuko cha m’madera ndipo mmalo mwawo ku unduna wa za umoyo kwapita a Chimpeni. Nduna zina zonse sizidasinthe mmipando mwawo.
A Chakwera adati mu 2024 dziko la Malawi lidalira kangapo monga pa imfa ya a Chilima ndi anthu ena 8 pa ngozi ya ndege, mphepo ya El-Nino yomwe idasokoneza zokolola ndi kupha anthu komanso kuononga chuma ndi mvula ya mkuntho yomwe idagwa mu December 2024 n’kuononga.
Komabe iwo adayamikira ntchito yomanga misewu, kukwenza ndalama ya CDF kufika pa K200 miliyoni ndikupezathandizo la ndalama zokwana K300 biliyoni zogulira chakudya choti boma lithandizire anthu 5.7 miliyoni omwe alibe chakudya.
M’ndemanga yake mkulu wabungwe la Centre for Social Transparency and Accountability a Willy Kambwandira adati: “Apulezidenti alankhula zopatsa chiyembekezo ngakhale mwina ndi mwina m’mafunikabe kulongosolera.”