Nkhani

A Chilima abwera poyera

Mtsogoleri wa chipani cha UTM a Saulos Chilima womwenso ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino dzulo aulula zomwe adagwirizana ndi mtsogoleri wachipani cha Malawi Congress Party (MCP) a Lazarus Chakwera omwe ndi mtsogoleri wadziko lino pa zomwe zili m’mgwirizano wao.

A Chilima adalankhula kwa pafupifupi ola limodzi ku Lilongwe kutsitsa chakumtima kwa Amalawi omwe adakhala akudikira mawu awo kuyambira Lolemba pomwe adalonjeza kuti alankhula.

A Chilima: Anati ndizichepetse

Mosapsatira, a Chilima adati mgwirizano wawo ndi a Chakwera  ndiwoti wina akatsogolera mu 2020,  ndiye kuti azasiira wina mu 2025.

“Mgwirizano wathu udali woti wina alamulira zaka zisanu (5) kenako adzapereka mpata kwa wachiwiri wake kuti naye adzalamulile zaka zisanu kuyambira 2025 ndipo ndimalandira anthu ine kundipempha kuti ndidzichepetse zomwe ndidachita,” adatero a Chilima.

Izi zikusemphana ndi zomwe akuluakulu ena achipani cha MCP monga wachiwiri kwa mlembi wake a Catherine Gotani Hara womwenso ndi Sipikala wa Nyumba ya Malamulo adanena kuti a Chakwera ndiwo adzaimilirenso mu 2025.

Potengera ndi mawu a Chilima, a Chakwera akhoza kudzaimanso pokhapokha atakhala pansi n’kukambirana zosintha mfundo za mgwirizano wawo kapena utatha kuti chipani chilichonse chiime pachokha.

Koma a Chilima adati alibe ganizo lotuluka mumgwirizano chifukwa safuna kunamiza Amalawi ndipo ngati pangafike poti mgwirizano uthe, pafunika kukhala pansi nkukambirana komanso kuitanitsa chisankho china polemekeza ufulu wa Amalawi.

“Apapa ngati mgwirizano ungathe, ndiye kuti pafunika chisankho china kuti yemwe azilamulira akhale osankhidwa ndi Amalawi chifukwa boma lomwe lilipo pano lidalowa ngati Tonse Alliance, kutanthauza kuti palibe yemwe ali ndi mphamvu zolamula kunja kwake,” adatero a Chilima.

Iwo adapempha anzawo amumgwirizano kuti ayenera kutsatira zomwe adapangana ndi kusainirana pakubadwa kwa mgwirizanowo posatengera kuti mphamvu ndi mipando zakoma.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu adakambaponso za kufunika kosintha gawo 91(2) la malamulo a dziko lino kuti pulezidenti naye azizengedwa mlandu akaswa lamulo ngakhale adakali pampando.

“Iyinso ndi mfundo mumgwirizano wathu kuti gawoli lidzasinthidwe kuti naye pulezidenti akalakwa, nthambi zofufuza ngati Anti-Corruption Bureau (ACB) zizikhala ndi mphamvu zomfufuza osaopsezedwa,” adatero a Chilima.

Iwo adati padakali pano, sanganene kalikonse pa zokhudzana ndi nkhani yakatangale ndi n’zika ya ku England a Zuneth Sattar chifukwa akufuna kutsata malamulo komanso sakufuna kusokoneza kafukufuku wa ACB.

Pazachuma, a Chilima adati mpofunika kulimbikitsa zomwe a Chakwera adanena zotsegula minda ya boma ndi misika kuti kupatula kutukula alimi, boma lizipereka ntchito m’madera a akumidzi.

Mneneri wachipani cha MCP a Maurice Munthali adati chipani chawo chikhala pansi kuti chiyankhe pa zomwe a Chilima adalankhulazo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button