Adzudzula MEC
Magulu osiyanasiyana okhudzidwa ndikayendetsedwe kazisankho adzudzula bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) posintha masiku odzachita kalembera wa kaundula wa chisankho.
Pa mkumano wa magulu osiyanasiyanawo monga zipani za ndale komanso mabungwe oima pa okha, wa pampando wa MEC mayi Annabel Mtalimanja adalengeza za kusintha kwa masikuwo.
Koma nthumwi zomwe zidali ku mkumanowo zidadzuma ganizolo ndipo ena adati ali ndi chikaiko kuti bungwe la MEC kudzayendetsa bwino chisankho cha 2025.
Atamva nkhaniyo, phungu wa pakati mu mzinda wa Blantyre a Chipiliro Mpinganjira adakumbutsa bungwe la MEC kuti ndi ntchito yake kuyendetsa chisankho mwa ukadaulo.
“Malingana ndi chiganulo cha khoti pa mlandu wa chisankho cha 2019, bungwe la MEC lili ndi udindo woyendetsa zisankho mokomera mbali zonse zokhudzidwa,” adatero a Mpinganjira.
Koma a Mtalimanja adatsimikizira nthumwizo kuti palibe chodetsa nkhawa ndi kusinthako chifukwa sizikhudza kalendala ya chisankho.
“Kusintha kwabwera chifukwa tikufuna kupereka mpata wa kalembera oyesa makina atsopano opangira kalembera omwe ndi apamwamba kwambiri kuti ngati pangakhale mavuto alionse, tithe kukonzeratu kalembera weniweni asadayambe,” adatero a Mtalimanja.
Iwo adati pa malamulo, MEC ikuyembekezeka kuyamba kalembera pakadutsa pa 16 September 2024 ndi kudzamaliza patsiku losadutsa pa 17 July 2025 kwa masiku 60.
“MEC ikuchita zotheka kuti kaundula wa chisankho adzakhale okomera aliyense ndipo chisankho chidzakhale cha chilungamo. Tikuyesetsa kupanga njira zoti aliyense azikhala okhutiira,” adatero iwo.
Mkulu wa bungwe lowona zachilungamo ndi Mtendere (CCJP) a Boniface Chibwana adati bungwe la MEC likuyenera kulengeza msanga masiku a kalembera kuti mabungwe ophunzitsa anthu za chisankho adzayambe ntchitoyo msanga.
Mlembi wamkulu wa ntahmbi ya za kalembera ya National Registration Bureau (NRB) a Mphatso Sambo ati bungwe lawo ndi lokonzeka kugwira ntchito ndi MEC kuti kalembera adzakhale wabwino.
“Tikulumikizana pafupipafupi ndi a MEC kufuna kuti tiziyendera limodzi. Mbali yathu tikuyesetsa kuti onse ofunika kulowa m’kaundula apatsidwe mpata ndipo tikuthamangathamanga,” atero a Sambo.
Iwo ati kuyambira chaka cha 2016, bungwelo lalemba Amalawi pafupifupi 12.3 miliyoni a zaka 16 ndi kuposera apo, kudutsa anthu 11.3 miliyoni amene amayembekezera kuwalemba.
“Izi zikusonyeza kuti tili ndi kuthekera kogwira ntchito imene tikuyenera,” adatero a Sambo.
Malinga ndi kupeza kwathu, anthu 9.2 miliyoni amene adzakwanitse zaka 18 kapena kuposera apo, kudazkhala ndi mwayi wovota pa chisankho.
MEC lakonza zochita kalembera woyeserera m’maboma a Chitipa, Dedza, Balaka, Neno ndi Nsanje komanso m’mizinda ya Mzuzu, Lilongwe ndi Blantyre.
Bungwelo lati, si kuti kalembera woyesererayu adzalowa m’kaundula weniweni wa mavoti a pa 16 September 2025.