Agwidwa ndi yunifomu za polisi
Abambo ena 8 adabwitsa anthu ku Chibavi, mumzinda wa Mzuzu atapezeka ndi yunifomu zapolisi.
Zovalazi ndi monga zigoba zovala panthawi ya zionetsero komanso za mphepo zolembedwa Malawi Police.
Pomwe Msangulutso unayendera kumalo komwe abambowo adagwidwa, anthu oyandikana nawo nyumba anati zachitikazo zawapatsa mantha.
Mmodzi mwa anthuwo a Madalitso Mzumara adati samadziwa kuti akukhala limodzi ndi anthu omwe akusunga katundu wa apolisi.
“Zatiopsa, ngati anakwanitsa kupeza zovala za apolisi ndiye kuti ifenso akanatha kutichita chipongwe,” anatero Mzumara.
Iwo anati izi zizichititsa kuti anthu azikaikira akaona apolisi ngati alidi achilungamo kapena onyenga.
Polankhulapo mneneri wa apolisi ku Mzuzu a Paul Tembo adatsimikiza kuti a Thomson Mbewe, a Chikondi Malinga, a Ramsey Chirwa, a Famous Nsani, a Jeremiah Banda, a Ladson Banda, a Alex Kavenji and a Gerald Mwale apezeka ndi yunifomu ya apolisi.
A Tembo adati anthuwo akuwaganizira kuti ndi omwe amasowetsa mtendere ku Chibavi.
“Anthuwa tawatsegulira mlandu wopezeka ndi katundu wakuba ndipo awonekera kubwalo la milandu masiku akubwerawa,” anatero a Tembo.
Iwo adati anthu akufuna kwabwino ndiwo adawatsina khutu apolisi kuti anthuwo ali ndi yunifomu za polisi.
Izi zachitika pomwe chitetezo chalowa pansi m’dziko muno ndipo ambiri akuloza zala apolisi kuti sakuchita zotheka pobwezeretsa chitetezo.
Nkhaniyi ili m’kamwa m’kamwa mwa Amalawi, bomba linanso laphulika kundende ya Chichiri komwe munthu wina anadzizimbaitsa ngati wapolisi n’kukatulutsa mkaidi kundendeko.
Nkhaniyi ikuti munthuyo anamutenga m’kaidiyo ponama kuti akupita naye kubwalo la milandu.
Ndipo mneneri wa ndende m’dziko muno a Chimwemwe Shaba kuti nthambi ya ndende ikufufuza za nkhaniyi komanso kufufuza komwe awiriwo adalowera.
Ndipo mphunzitsi wa za chitetezo pa sukulu ya Mzuzu University a Aubrey Kabisala anati kupezeka ndi yunifomu zapolisi kukutanthauza kuti anthuwo ali ndi cholinga chomadzizimbaitsa ngati apolisi.
Iwo adati izi zikutanthauza kuti ukadaulo wa umbanda ndi umbava wafika pa mlingo wina chifukwa azichita moonetsera moti anthu sangadziwe kuti ndi mbava mwachitsanzo: pomaima pamsewu kuimitsa galimoto, kumapita m’midzi yakutali kukalanda katundu podzizimbaitsa ngati apolisi.
“Akhoza kupita m’misika yakutali ngati apolisi oyenda mongoyerekeza ndi bungwe lotolera misonkho la Malawi Revenue Authority(MRA) n’kulanda anthu katundu kumeneko, anthuwo mosadziwa n’kumati ndi apolisi. Apapa tingoti anthuwo ali n’kuthekera kogwira ntchito ngati apolisi amene,” anatero a Kabisala.
Iwo analangiza apolisi kuti mpofunika kuphunzitsa anthu mwakathithi kupempha kuona chiphaso cha wapolisi kapena kufunsa nambala yake ya kuntchito kuti azitsimikizadi ngati ali wapolisi.
“Vuto ndi loti ambirife timakhala ndi mantha, timaopa kuti apolisiwo ationa ngati ndife achipongwe ndipo tikumana ndi mavuto,” iwo adatero.
Apa a Kabisala adatinso anthu akhozanso kupempha apolisi omwe akuwakaikira kuti ngati pali milandu akakambire kusiteshoni ya polisi pofuna kudziteteza ku mbava zodzizimbaitsa ngati apolisi.