AIP yadza nzakenso
Unduna wa za malimidwe udati alimi ayamba kugula zipangizo za ulimi zotsika mtengo sabata yomwe ikuthayi koma Tamvani wapeza kuti m’madera ena zipangizo zidafika pomwe kwina sizidafike.
Chithunzithunzichi chaoneka pofuza kupyolera mwa atolankhani athu a m’madera m’dziko muno.
Mafumu ena nawo apereka chithunzithunzi cha momwe akuiwonera pulogalamu ya AIP ya chaka chino ndipo asonyeza kuti pena chiyembekezo chilipo pomwe pena zikudetsa nkhawa.
Unduna wa za malimidwe udalengeza kuti chaka chino alimi opindula mu AIP alipo 1 054 945. Mwa awa, alimi 1 048 445 ndiwo adzapindule ndi zipangizo monga fetereza ndi mbewu pomwe alimi 6 500 a m’maboma a Balaka ndi Mwanza adzalandira mbuzi ziwiri zazikazi.
Chiwerengero cha olandira zipangizozi m’boma la Mchinji chachoka pa 60 000 kufika pa 43 000 ndipo misika ilipo itatu ku Mikundi, Tembwe ndi Mchinji Boma.
Mmodzi mwa opindula pa chilinganizochi m’bomalo mayi Magaleta Zulu ati dzina lawo lili ndi mavuto ena m’kaundulamo. “Nambala imene ili m’kaundula ikusiyana ndi nambala ya chitupa change. Ndakhala ndikuyendera za vutoli koma akungondiuza kuti akuzikonza ku Lilongwe.
Mkulu wa zaulimi m’bomalo a Hastings Yotamu adati ntchitoyi ikuyenda mwa pang’onopang’ono koma iwo sanalandire.
Ndipo titayendera msika wa Tembwe tidapeza anthu akudikira maola angapo kuti athe kugula fetereza ndi mbewu zotsika mtengo.
Mmodzi mwa anthuwo, mayi Martha Jere adati: “Ndatenga mphindi 30 akundijambula koma kenako adati pali vuto la netiweki. Bola ine ndabwera lero koma anzanga awiriwa anakumana ndi mavuto omwewanso dzulo.”
Wapampando wa komiti ya pampando wa pulezidenti ku chipaniko n’kufuna kuti UTM idzakhake ndi mphamvu zambiri pa chisankho cha 2025.
“Pano ndafika mpamphambano chifukwa kolowera n’komwe kunganene tsogolo la chipani ndi dziko la Malawi. Chondilimbitsa mtima kwambiri ndi masomphenya a chipani cha UTM. Sitikufuna kungotenda utsogoleri wa mphamvu wa chipani koma utsogoleri omwe udzatukule ndi kukomera Amalawi onse pothetsa mavuto awo choncho ndikupempha kuti paulendowu mukhale nane limodzi,” adatero a Kabambe.
A Mtumbuka nawo adakapereka kalata zawo ndipo iwo adapempha nthumwi zomwe zikasankhe atsogoleri ku konvenshoni kuti akapewe kusankha atsogoleri osinthasintha mawanga.
Iwo adati nthawi ino ndi yofunika atsogoleri achinyamata omwe nzeru zawo n’zautsigoleri wokomera dziko lonse osati atsogoleri a mtima ogofuna kudzitukula okha kuiwala dziko lawo.
“Dziko la Malawi likufunika mtsogoleri yemwe ali ndi ukadaulo otha kuyendetsa dziko ngati kampani, mtsogoleri wofuna kunka chitsogolo ndi woika mtima wa dziko lonse kuposa chilichonse,” adatero a Mtumbuka.
Nawo adati ndi wokonzeka kudzabweretsa utsogoleri watsopano komanso kudzaonjezera mphamvu ndi chikoka cha UTM pa chisankho cha 2025 kenako n’kudzalamulira moluzanitsa Amalawi onse. Sabata yatha padali mpungwepungwe pomwe mlembi wamkulu wa chipanicho a Kaliyati adamangidwa kutatsala tsiku limodzi kuti komiti yaikulu ya chipanicho ikumane koma mkumanowo udapitirira ngakhale kuti a Usi womwe amayenera kutsogolera sadapiteko.