Nkhani

Ofuna utsogoleri wa UTM apereka zikalata

Pamaoneka gwedegwede wokhudza msonkhano waukulu wa chipani cha UTM koma tsopano zaoneka kuti mutu wa konvenshoniyo ilikoliko pa 17 November 2024.

Izi zatsimikizika Lachitatu pomwe ena mwa omwe akufuna utsogoleri wa chipanicho monga a Mathews Mtumbuka komanso a Dalitso Kabambe adapereka zikalata zawo ku likulu la chipanicho mu mzinda wa Lilongwe.

Chosangalatsa n’choti onse awiri adapereka uthenga wa utsogoleri wa ngwiro komanso wofuna kutukula Malawi ndi kutsogolera UTM ku chipambano mu 2025.

Chipanicho chidati ofuna mpando wa upulezidenti akuyenera kupereka K20 miliyoni ndipo anthu asanu ndi mmodzi ndiwo adaonetsa chidwi chofuna mpandowo.

Anthuwo ndi Michael Usi omwe ndi wachiwiri kwa pulezidenti wa dziko komanso pulezidenti wa UTM, mayi Patricia Kaliati omwe ndi mlembi wamkulu wa chipani, a Mtumbuka komanso a Dalitso Kabambe omwe adakhalako gavanala wa banki yaikulu, a Newton Kambala komanso mkulu wa achinyamata m’chipanicho a Penjani Kalua.

Oyamba kukapereka kalata adali a Kabambe omwe adauza anthu adawaperekeza kuti cholinga chawo popikisana nawo chitukuko kumeneko a Rodgers Chizizi ati alandira madandaulo angapo otere koma palibe icho angachite.

T/A Nyoka ya m’bomalo adati boma lichite machawi pa chilinganizochi popewa izo zidachitika chaka chatha pofuna kupewa zovuta zimene zidalipo chaka chatha.

Ndipo mkulu wa za ulimi m’boma la Mwanza a Feston Kwezani Lachiwiri adati anthu 4 195 ndiwo akuyembekezereka kupindula ndi chilinganizochi m’bomalo koma matumba 859 a feterza wa chitowe ndi 750 a urea ndiwo adagulidwa m’misika ya Mwanza Boma, Tulonkhondo, Kunenekude ndi Thambani.

“Tikufuna kuti msika wina utsegulidwe m’mudzi mwa Kabango ndiye zidzathandiza kuti tikhale ndi misika iwiri mu dera lililonse la phungu m’bomali, atero iwo.

Atolankhani athu a m’maboma a Salima ndi Chitipa adati kwawoko ntchitoyi siyidayambe ngakhale malo ogulitsira adakonzedwa kale.

Nako ku Kasungu, mfumu yaikulu Njombwa yomwe dera lake pulogalamu ya AIP idayambira chaka chatha idati kugulitsa zipangizo sikudayambe kwenikweni koma masitepe ena akuchitika.

“Misika idakonzedwa, ogulitsa zipangizo adabwera kale ndipo anthu akumakaona maina ngati ali m’gulu lopindula koma fetereza ndi mbewu tikuziyembekezera sabata ikubwerayi,” adatero a Njombwa.

Mfumu yaikulu Mwankhunikira ya m’boma la Rumphi idati zipangizo sizidayambe kugulitsidwa ndipo idati nkhawa yaikulu ndi kuchepa kwa maina omwe akupezeka pamudzi.

“Akuti idzayamba posachedwa koma maina atuluka ochepa kwambiri moti m’midzimu anthu ayambanamo chifukwa ena omwe adali mndondomeko koma pano adawachotsamo ndiye kuli mkwiyo waukulu,” adatero a Mwankhunikira.

Nduna ya za malimidwe a Sam Kawale adati chilichonse chokhudza AIP chili m’chimake ndipo zipangizo ziyamba kutumizidwa m’madera ovuta kufikamo kuti mvula ikamabwera, m’madera otero zipangizo zikhale zitafika.

“Makampani ogulitsa tidawapeza kale, galimoto zonyamula zipangizo zidapezeka kale komanso fetereza ali kale m’dziko momwe muno pomwe wina ali kudoko. Fetereza wina agulidwa mu ndondomeko ya chaka chino pomwe wina ndi yemwe adatsala chaka chatha,” adatero a Kawale.

Pano mvula yagwa m’madera ena ndipo alimi akangalika kale m’minda yawo koma kupatula kudalira fetereza, alimi ambiri adapanga manyowa potsatira langizo la akadaulo ndi unduna wa za malimidwe potengera kuti fetereza adabwera mtengo. Koma polingalira kuti alimi ambiri sadakolole bwino chaka chatha, unduna wa za malimidwe udalengeza kuti mtengo womwe alimi amawombolera zipangizo chaka chatha siudasinthe kuti alimi ambiri asapsinjidwe.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button