Amalawi abwerera kumsewu

Amalawi ena amene akufuna kuti wapampando wa bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah atule pansi udindo, dzulo adachita zionetsero zina m’madera ena a dziko lino.

Polankhula ndi Tamvani kumayambiriro a zionetserozo mumzinda wa Lilongwe, wapampando wa mabungwe omwe akutsogolera zionetsero za dziko lonse la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) Timothy Mtambo adati adakhutira ndi momwe anthu adatulukira kukaonetsa mkwiyo wawo.

Iye adati: “Zomwe Amalawi achita lero n’zotamandika kwambiri ndipo wakumva akuyenera kumva n’kupanga zomwe eni dziko akufuna. Nkhani yathu yaikulu ndi yomwe ija, Jane Ansah atule pansi udindo chifukwa wasonyeza kulephera.”

Mtambo adati ngati Ansah satula pansi udindo potsatira chionetsero cha dzulo, zionetsero za Lachiwiri ndi Lachisanu sabata iliyonse zipitirira mpaka Amalawi adzayankhidwe.

“Sitigonja ndipo sitikuopa. Tizipanga zionetsero mpaka madandaulo athu amveke ndipo nkhawa zathu ziyankhidwe,” adatero Mtambo.

Zionetserozo zidachitika m’maboma ambiri kuphatikizapo ku Chitipa komwe chifukwa cha mkwiyo, Amalawi adalimbana ndi apolisi omwe amakhazikitsa bata ndipo mwa zina adaphwanya ofesi ya zankhalango m’bomalo.

Ndipo ku Blantyre, otsatira chipani cha DPP ena adamenyedwa ndi asirikali pomwe amafuna kusokoneza ofuna kuyendawo. Kumayambiriro, khonsolo ya mzinda wa Blantyre imaletsa zionetsero ati chifukwa khonsolo ya mzindawo imasankha mfumu ya mzindawo.

Pomwe timasindikiza nkhaniyi dzulo masana, n’kuti zionetsero zili mkati mumzinda wa Mzuzu ndipo tidalandira malipoti kuti ena adaphwanya sitolo ya Chipiku.

Ansah adanenapo mmbuyomo kuti anthu akungovutika kupanga zionetsero chifukwa iye sangatule pansi udindo wake pokhapokha yemwe adamuika pampandopo yemwe ndi Pulezidenti atamuchotsa.

Polankhula sabata yatha otsatira DPP atachita zionetso zosangalala kuti DPP idapambana chisankho, Mutharika adaopseza kuti athana ndi aliyense yemwe azipanga zionetsero.

Sitolo zina zinali zotsekedwa m’mizinda ya Blantyre ndi Lilongwe ndipo makolo ena sadatumize ana awo kusukulu poopa zochitika kumsewu.

M’kalata yomwe idaperekedwa dzulo, anthu ochita chionetserowo adadandaulamo za imfa za anthu 6 omwe amakhudzidwa ndi zachisankho omwe adafa mwadzidzidzi kuchokera pa 21 May tsiku lachisankho.

Kadaulo pa ndale George Phiri adati mfuwu wa Amalawi wamveka mokwanira kudzera m’zionetsero ndipo adati Mutharika ndi Ansah akuyenera kuchitapo kanthu zinthu zisadafike poipa.

Iye adadzudzula mchitidwe woopseza anthu ochita zionetsero ponena kuti kuteroko n’kuwaphwanyira ufulu omwe malamulo adziko lino amapereka kwa anthu.

Share This Post