Nkhani

Amanga mbusa wogwirira mwana

Apolisi m’boma la Chiradzulu Lachinayi adamanga mbusa wina wa zaka 35 pomuganizira kuti anagwirira mwana wa zaka 16 yemwe ndi chiwalo cha mpingo wake.

Mneneri wapolisi ya Chiradzulu a Cosmas Kagulo ati mbusayo ndi a Shazira Bvumbwe ndipo akuwaganizira kuti akhala akupalamula mlanduwo kuyambira mu August chaka chino.

A Kagulo anati zadziwika kuti mbusa Bvumbwe anasiyana banja ndi mkazi wake ndipo analamula azimayi mu mpingowu kuti azitumiza atsikana ku nyumba kwake kuti azidzagwira ntchito za pa khomo.

A Kagulo anati litafika tsiku loti mtsikanayo akagwire ntchito ku nyumba ya munthu wa Mulunguyo, iye anamunyengerera kuti agone naye ndipo anamulonjeza kuti adzamukwatira mtsogolomo.

A Kagulo anati ichi chinasanduka chizolowezi mpaka Bvumbwe anapereka mimba kwa mtsikanayo.

“Nkhani ya mimba itadziwika makolo anakasiya nkhaniyo ku polisi ya Milepa ndipo mtsikanayo anamutumiza ku chipatala chaching’ono cha Milepa komwe atamuyeza anatsimikiza kuti ali ndi mimba. Apa tidamugwira ndipo titamufunsa adakana nkhaniyi ponena kuti mtsikanayo anamuuza kale,” atero iwo.

Ndipo a Kagulo ati woganiziridwayu akuyembekezera kukaonekera pa bwalo la mlandu posachedwapa kuti akayankhe mlandu wogonana ndi mwana.

Mbusayo amachokera kwa Jombo T/A Ngabu m’boma la Chikwawa.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button