Mayi adzipha ku Mulanje
Mayi wina wa zaka 29 wadzikhweza ndi nsalu ku denga la nyumba yake pa zifukwa zomwe sizikudziwika ku Mulanje.
Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Mulanje mayi Leah Chagomerana ati malemuwa ndi a Chinsinsi Nalitsiro omwe adadzikhweza pa 10 October 2024 pa mudzi wa Chimtengo kwa T/A Juma m’bomalo.
A Chagomerana anati patsikulo m’mawa malemuwa anachoka ku nyumba kwawo kupita ku dimba kwawo komwe amakathirira ndipo anabwererako dzuwa likuswa mtengo 12 koloko masana.
A Chagomerana anati atafika ku nyumba malemu a Nalitsiro anakonza chakudya chake ndi ana ake omwe panthawiyo anali ku sukulu.
A Chagomerana anati anawa anabwererako ku sukuluko cha m’ma 2 koloko masana ndipo anapeza mayi awowo atadzimangirira ku denga m’chipinda mwawo.
Iwo anati nkhaniyo anakasiya ku polisi yaing’ono ya Namphungo ndipo a polisi ndi a chipatala cha Namphungo anathamangira ku malowa ndi kutsimikiza kuti malemuwa anamwalira kaamba kobanika.