Nkhani

Amuna anga matama thooo!

Azakhali, zili kwathu simungazimvetse. Ife tonse tili pa ntchito. Tonse timalandira ndalama zokwanira ndithu.

Komwe ndalama za amuna anga zimapita sindidziwako. Nthawi zonse amati ali ndi ngongole ku ntchito.

Ine ndidagula galimoto yanga ndipo nawonso adagula yawo. Koma iwo nthawi zones amangoti ndili ndi ngongole ya galimoto. Kuwafunsa kuti kodi ngongoleyo idzatha liti, amangoti ndi yaitali.

Kuti asamale pakhomo zimawavuta. Chomwe amadziwa ndi kukamwera mowa wodula ku malonso a pamwamba. Komanso amadzipangitsa kukhala andalama pa maso pa abale awo ndi anzawo.

Ndi munthu woti sindimamumvetsetsa. Anatche, tanganizani kuti kumuuza kuti tiyeni tigule malo kuti timange nyumba amanena kuti alibe ndalama chifukwa choti ali ndi ngongole ku ntchito.

Ine ndidamanga nyumba ndekha. Iwo amawauza anzawo kuti nyumba adamanga ndi iwowo akuti chifukwa ndi mwamuna ndiye ine ndikamanena kuti ndidamanga ndekha ndiye kuti ndikuwachotsa ulemu.

Zitandinyansa ndidapita kukanena kwa makolo awo pa zimene amachita. Makolo awo adandiuza kuti ndisazitengere zomwe amachita amuna angawa.

Ndidawafunsa makolowa ngati amathandizidwa ndi mwana wawoyo, iwo adati sawathandiza akuti chifukwa makolowa amagwira ntchito ndiye palibe chifukwa choti aziwathandizira. Apa ndi pamene ndidazindikira kuti amuna anga alibe mdalitso.

Adandiuza kuti ndizilimbikira kupemphera ndikumupempherera komanso ana athu kuti asadzatenge mtima wa bamboo awo.

Azakhali, kodi pamenepa banjali lipitirire? Ndichite bwanji ine?

Inewodandaula,

Lilongwe.

Zikomo mayi,

Banja ndi chinthu chabwino kwambiri. Koma anthu ambiri timalichititsa kuti likhale loipa. Zikuonetsa kuti amuna anu mutu wawo siumagwira.

Mwamuna amayenera kuonetsa kuti ndi mwamuna pa chilichonse ngati ali ndi kuthekera. Iwo ali ndi kuthekera koma akufuna kukhala m’khwapa mwa mkazi.

Kubadwa mopusa kumeneko. Mowa omwe akumwa odulawo ndi anzawo ndi osapindula pa iwo. Palibe yemwe angawatame kuti amamwa mowa odula ayi. Adzalira patsogolo.

Chomwe ndingakuuzeni n’choti pitirizani kuchita zitukuko zanu kuti ana anu asadzavutike. Osaiwala kusunga pabwino malisiti a zomwe mumagula komanso azikhala m’dzina lanu.

Amuna anu akuoneka kuti ndi aupandu. Muthanso kusintha mapepela a nyumba yanu ndi kulemba maina a ana anu kuti adzasowe chonena kuti ndi zawo.

Amenewadi ndi wofunika mapemphero kuti asinthe.

Anatchereza.

Ngati muli ndi mavuto alionse ndipo mukufuna muthandizidwe, tumizani uthenga wa palamya ku 0888 187 414. Chonde, osaimba panambala iyi.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button