‘Samalani m’masamba a mchezo’
Mkulu wa bungwe loteteza ufulu wa ana ndi achinyamata a MacBain Mkandawire wapempha Amalawi kuti azigwiritsa ntchito masamba a mchezo moyenera chifukwa akhoza kupalamula milandu ingapo.
A Mkandawire anena izi titawafunsa ndemanga yawo pomwe sabata yatha apolisi mu mzinda wa Blantyre adaitanitsa mtsikana wa zaka 11 yemwe ali Sitandade 7 ndi kumulangiza kuti aleke kutulutsa mavidiyo amene si a msinkhu wake. Apolisiwo adaitanitsa mtsikana yemwe amadzitcha kuti Ndaziona ndipo zisudzo zake amati Makilinyombe Comedy limodzi ndi manijala wake a Kenfold Chipelesa omwe amatchuka kuti Ken B Wazakena m’masambawo.

M’makanemawo, Ndaziona wakhala akumachita zisudzo zolimbikitsa atsikana kuchita za dama ndi zidyamakanda. Koma apolisi amuitanitsa adamulangiza kuti aleke izi chifukwa n’kuphwanya ufulu wa atsikana amene angatengeke ndi zimene amafalitsazo.
Mneneri wa polisi ya Blantye, a Peter Mchiza adati kulola ana kuti achite zinthu zoposera msinkhu wawo monga momwe amachitira mtsikanayo ndi zosemphana ndi malamulo a dziko lino ndipo munthu akapezeka akuchita izi pamayenera kuti lamulo ligwire ntchito yake.
“Kuika mavidiyo omwe amachita zoposera msinkhu wake ndi kuphera ufulu wa ana ndipo ife ngati apolisi ndi udindo wathu kuonetsetsa maufulu a anthu akutetezeka. Ichi n’chifukwa tinaitana manijala wakeyo kuti tiwalangize za izi kuti aziika mavidiyo abwinobwino osati obweretsa mafunso pamaso pa anthu m’dziko muno,” adatero iwo.
Pophera mphongo, a Mkandawire ati bungwe lawo likupitiriza kugwira ntchito ndi nthambi ya boma yoyang’anira zofalitsa mauthenga ya Macra kuti aonetsetse kuti pa masamba a mchezo sipakuyenda nkhani komanso mauthenga omwe ali ophera ufulu ana m’dzikomuno, zomwe akuzitcha Child Online Abuse Prevention m’Chingerezi.
“Mwana amayenera kutetezedwa ku mauthenga omwe siogwirizana ndi msinkhu wake monga mmene limanenera lamulo lalikulu la dziko la Malawi pa nkhani ya maufulu a ana,” atero a Mkandawire.
Iwo alangizanso anthu kuti asamagundike ndi kupititsa nkhani pa masamba a mchezo akayambana kumbali pa nkhani zosiyanasiyana, poti uku ndi kusagwiritsa bwino ntchito makina a Intaneti.
“Ngati anthu ayambana asapititse nkhani pa Intane tikuti akatukwana kapena kumuyalutsa mnzawo pagulu chifukwa munthu onyozedwayo akadandaula, bungwe la Macra limatengapo gawo potsatira malamulo a dziko lino kuti sikoyenera kumuipitsira mbiri mnzako,” atero a Mkandawire.
Iwo ayamikira apolisi posamanga mwanayu koma kungomulangiza kuti ayenera kusiya kupanga mavidiyo oterewa poti sikoyenera potengera malamulo kuti amange mwana osamulangiza kaye.
Mkulu wa Macra a Daud Suleman Lachiwiri adati anthu asiye kugwiritsa ntchito masamba amchezo mosayenera popeza lamulo ligwira ntchito kwa amene angapezeke akuchita izi.
A Suleman adati malamulo sasankha munthu akapezeka wolakwa pa mlandu osagwiritsa ntchito bwino masamba a mchezo.
“Anthu asiye kugwiritsa masamba a mchezo molakwika. Malamulo alipo omwe amabwalo a milandu amaagwiritsa ntchito,” atero iwo.
Komanso a Suleman anati anthu ogwiritsa ntchito masamba a mchezo asamatengeke ndi zinthu zina zomwe zingawaike m’mavuto ngakhalenso kuwaika pa chiopsezo choti atha kuberedwa.
Iwo anati masiku ano kwachuluka zigoba pa masamba a mchezo, zomwe zikumanamizira kukhala anthu ena ndi cholinga chowabera anthu osadziwa.
Mmodzi mwa akatswiri pankhani za kagwiritsidwe ntchito ka makina a Intaneti, a Bram Fudzulani, ati anthu akuyenera kuti azidziwitsidwa pafupipafupi za njira zimene akubawa akumagwiritsa ntchito kuti azipewa kuberedwa kudzera pa makina a Intaneti pozindikira kuti akubawa amasinthasintha njira zofuna kubera anthu pafupipafupi.
“Zimavuta kuthetsa nkhani zobera nakudzera pa makina a Intaneti kaamba koti amene amapanga izi amasintha njira zawo pafupipafupi ndipo amayesetsa nthawi zambiri kuti azikhala patsogolo ndi iwo maka popanga njira za tsopano zobeea anthu pa masamba a mchezo,” atero iwo.
Iwo alangizanso anthu kuti asamakonde kudina malinki pofuna kulandira zinthu zaulele chifukwa zambirinso zomwe zikuchititsa kuti anthu aberedwe kudzera pa Intaneti ndi kudina malinki omwe amanena zoti munthu apeza ndalama kapena mabandulo a Intaneti mwaulele.