Nkhani

Ana akagonana azimangidwa?

Listen to this article

Bwalo lalikulu la milandu Lachitatu likudzali likhala likumva mlandu umene mnyamata wina wa zaka 15 (sitimutchula dzina) wasumira boma.

Mnyamatayo adakamang’ala kubwalolo apolisi adamugwira ndi kumuzenga mlandu woti adagona ndi mwana.

Chijozi: Anyamata okha ndiwo amamangidwa

Gawo 138 (1) la mnalamulo a dziko muno limati ndi mlandu kugona ndi mwana wa zaka zosaposa 16 koma mnyamatayo akufuna kumvetsetsa ngati apolisi ali ndi mphamvu yomanga mnyamata yekha ana atagwirizana zokhalira malo amodzi.

Woimira mwanayo ndi a Chikondi Chijozi komanso a Ruth Kaima mmalo mwa bungwe lounika za malamulo kummwera kwa Africa la Southern African Litigation Centre (SALC). Iwo akufuna bwalolo liunikire ngati mlandu wa mwanayo ungapitirire kubwalo la majisitiliti.

A Chijozi adati cholinga chawo n’kuteteza ana aamuna.

“Ana okulirapo amapanga zibwenzi ngati ana okhaokha, koma masiku ano anawa akagwidwa, mwana wa mwamuna yekha ndiye akumamangidwa. Ife tikufuna khoti liunike bwino pamenepa,” adatero a Chijozi.

Iwo adati akufuna kuti papezeke njira zina zolangizira anawa osati kukalowa kundende.

“Mlandu uzikhalapo ngati mwana wokulirapo mwina wa zaka 15, wagwiririra mwana wochepa msinkhu koma osati kuzenga milandu ana oti adali pa ubwenzi wogonana,” iye adalongosola.

Mlanduwu walowa khoti pomwenso pa June 21, mwezi watha, bwalo la milandu la majisitiliti mumzinda wa Blantyre lidagamula kuti mnyamata wina wa zaka 18 yemwe adali pa ubwenzi wogonana ndi mtsikana wina wa zaka 15 alibe mlandu wogwiririra.

M’chigamulocho, woweruza milandu a Elijah Blackboard Dazilikwiza Daniels adauza a boma kuti amutulutse kundende mnyamatayu komwe adakhalako kwa miyezi 8, chim’mangireni chaka chatha chifukwa adalibe mlandu uliwonse.

Mmodzi mwa omenyera ufulu wa ana, a Desmond Mhango adauza wailesi ya Capital FM mkati mwa sabatayi kuti  anawa asamatumizidwe kundende pa nkhanizi.

Iwo adati lamulo logwiririra ana limati munthu wamkulu amangidwe akamagona mwana wamg’ono.

“Ndi zodabwitsa kuti anawa akumazengedwa milandu m’makhoti akuluakulu osatinso makhoti a ana,” adatero a Mhango.

Related Articles

Back to top button
Translate »