Nkhani

Apempha zipani kuthandiza a ulumali

Mkulu wa bungwe la Disability HIV/Aids Trust yomwe ndi nthambi ya Federation of Disability Organizations in Malawi (Fedoma) a David Njaidi apempha zipani kuti zithandize anthu aulumali omwe ali ndi chidwi chodzapikisana nawo pa mipando yosiyasiyana pa chisankho cha pa 16 September chaka chino.

Iwo ati ndi zomvetsa chisoni kuti nthawi zambiri zipani zimalephera kupereka thandizo lokwanira kwa anthuwa zomwe zimachititsa kuti aulumali ambiri asamatenge nawo gawo pa nkhani za ndale.

Happy to be housed in a secure environment

Koma iwo adati pofuna kulemekeza mfundo za demokalase, zipanizi zikuyenera kuthandiza anthuwa monga momwe zichitira ndi anthu alunga.

“Anthu aulumali amakumana ndi mavuto kuti adutse pa zisankho zachipulula ngakhale chisankho chachikulu kaamba kosowa thandizo kotero tikupempha zipani kuti zithandize anthu aulumali omwe awonesa chidwi chozapikisana nawo pazisankho za chipulula komanso chisankho chachikulu chomwe chili patsogolo pathu,” adatero iwo.

Naye mkulu wa bungwe la Fedoma a Symon Munde adapempha bungwe loyendetsa chisankho la MEC kuti lizifunsa maganizo a anthu a ulumali panthawi yomwe akusankha malo ochitira ntchito ya chisankho pofuna kuonetsetsa kuti akutsatira njira zolemekezera ufulu wa anthu a ulumali.

“Monga anthu aulumali pamodzi ndi mabungwe omwe amatiimirira kuphatikizapo bungwe lathu la Fedoma tidatsatira ndondomeko ya kalembera momwe inayendera ndipo tidapeza kuti malo ambiri sadali ofikilika (osayenera) kwa anthu aulumali. Kotero ngati izi sizingasithe ambiri mwa anthu aulumali agwa mphwayi zomwe zipangise kuti asatenge nawo gawo lokavota,” adatero a Munde.

Kumbali ya anthu aulumali omwe awonesa chidwi chozapikisana nawo pamipando yosiyasiyana m’zipani yosiyasiyana, a Munde adati pakadali pano anthu osachepera 50 ndiomwe awonesa chidwi chozapikisana pamipando yaukhansala komanso pamipando ya aphungu anyumba yamalamulo.

Wachiwiri kwa mlembi m’chipani cha United Democratic Front (UDF) a  Labana Chilunga adati chipani chawo chimakhulupilira kuti anthu a ulumali ndi anthu a chilungamo ndi odalilika pachitukuko kotero chimathandi komanso kulimbikisa anthu ochisatira chipanichi kuti azivotera anthuwa.

“Ngati njira yothandizila anthu a ulumali omwe akupikisana pamipando yosiyasiyana tidasisa mitengo yomwe anthu opikisana pachisankho akuyenera kulipila mwachitsanzo kwaomwe akupikisana pa mpando waaphungu anyumba yamalamulo amuna akupereka K150 000 malo mwa K300 000, mpando wakhansala akulipira K50 000 malo mwa K100 000.

“Pomwe amayi omwe akupikisana pamipando yaukhansala akupereka K25 000 malo mwa K50 000 ndipo omwe akupikisana pamipando ya aphungu anyumba yamalamulo akupereka K75 000 malo mwa K150 000. Zonsezi ndi chifukwa choti timakhulupilira kuti anthu a ulumali ali n’kuthekera kokhala atsogoleri abwino,” adatero a Chilunga.

Ndipo mneneri m’chipani cha UTM a Felix Njawala ati chipanichi chikuchita chilichonse pothandiza anthu omwe akupikisana nawo pa zisankho zachipulula komanso chisankho chachikulu kuzera njira zamauthenga komanso upangiri.

“Ndi zoona kuti anthu aulumali amafunikira thandizo ndipo ngati chipani tikuchita chilichonse powathandizira munjira yosiyasiyana. Chithu china chosangalasa ndichakuti anthu omwe akutenga mbali yopikisana pamipando yosiyasiyana kuchipanichi koma ndi aulumali, ndi anthu ozilimbikira kwambiri, ndipo adazimenyera kale nkhondo,” adatero a Njawala.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button