Nkhani

Apha mkazi wake kaamba ka nsanje

Listen to this article

Akuluakulu amati pali nsanje pali chikondi, koma zina zinyanya.

Nsanje zina zimaonjeza ndipo zimasanduka chiopsezo pa miyoyo ya anthu ena.

Monga zakhalira m’boma la Dedza komwe bambo wina wapha mkazi wake pomukhapakhapa chifukwa cha nsanje.

Ndipo chisoni chakuta mudzi wa Lumwira kwa Mfumu Kasumbu, m’bomali chifukwa cha imfa ya Sipeniya David wa zaka 35.

Malinga ndi mneneri wapolisi m’bomalo Cassim Manda, Kasumbu adaphedwa usiku wa Lamulungu, kucha kwa Lolemba.

Manda adati iwo ngati apolisi, omwe adaona thupi la David, akuchita kukanika kulongosola momwe Simthawika Sibombe wa zaka 40 adamukhapira mkazi wakeyo.

Manda adati Sibombe yemwe amachokera m’mudzi mwa Chiphuka kwa Mfumu Kasumbu komweko, adakwatirana ndi David zaka 7 zapitazo.

“Koma banjali silimamvana chifukwa Sibombe amamuchitira mkazi wakeyo nsanje yodabwitsa,” adalongosola Manda.

Iye adati zonse zidayamba Lamulunguli, nthawi ili cha m’ma 4 koloko masana pomwe David adali paulendo wopita kokazonda mchemwali wake yemwe adagonekedwa pachipatala cha Kanyama chomwe chili m’deralo.

“Apa mwamuna wakeyu yemwe adam’bisalira David pa manda ena omwe ali m’deralo, adavumbuluka ndikufikira kumukhapa mkaziyu manja onse komanso m’mutu. David adafera pomwepo pomwe Sibombe adathawa atangochita izi,” adalongosola motero Manda.

Iye adati Sibombe sadapezekebe mpaka pano ngakhale apolisi amutsekulira mlandu wopha munthu mosemphana ndi gawo 209 la malamulo a dziko lino.

Awiriwo ali ndi ana awiri.Chiwerengero cha anthu ophana chakhala chikukwera m’boma la Dedza chifukwa m’chaka cha 2018, anthu 20 ndiwo adaphedwa pomwe anthu 31 adaphedwa chaka chatha.

Related Articles

Back to top button