Aphungu akwangula
Aphungu a Nyumba ya Malamulo adakwangula zokambirana zawo dzulo Lachisanu atadutsitsa bajeti yokwana K5.98 triliyoni yomwe akadaulo adati ithandiza kusoka mabala akugwa kwa Kwacha.
Koma ngakhale zokambiranazo zidatha, m’nyumbayo mudali mikangano yokhayokha moti pena ndi pena a sipikala amapereka zilango zoti asaonekere m’nyumbayo.
Phungu wa dera la kummwera cha kummawa kwa boma la Blantyre a Sameer Suleman a chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) Lachitatu adapatsidwa chilango chosakambirana nawo Lachinayi.
Iwo adapalamula mlandu wofuna kumenyana ndi phungu mnzawo a Mark Botomani a dera la Zomba Chisi atasemphana maganizo pa nkhani yoti Nyumba ya Malamulo ikambirane zokhazikitsa mlingo wa zaka omwe munthu angayime ngati Pulezidenti komanso phungu pa chisankho.
“Bilu imene ija ndi yosaka munthu osati ya chilungamo. Malamulo a dziko lino amati aliyense ali ndi ufulu wotenga mbali pa ndale kapena kukhala paudindo ndiye lero tiyambe kuika malire kwa anthu? Zimenezo n’zosamveka,” adatero a Suleman.
Nkhaniyo idayamba nthawi yopumulira pomwe pungu wakummwera kwa boma la Chitipa a Welani Chilenga adasonyeza kuti ankafuna kukayambitsa nkhaniyo m’nyumbayo koma aphungu ena adamulezetsa mtima.
Aphunguwo atabwerera, a Suleman ndi a Botomani sadamvane pa za biluyo mpakana kufuna kumenyana koma aphungu anzawo adawagwira ndipo wachiwiri kwa wachiwiri kwa Sipika a Aisha Mambo Adams adaimitsa zokambiranazo.
Iwo ataunika nkhaniyo, adagwiritsa ntchito gawo 105 ya malamulo a Nyumba ya Malamulo n’kugamula kuti a Suleman asatenge gawo pazokambirana za Lachinayi pomwe a Bottoman adawagamula kuti asatenge gawo Lachinayi ndi Lachisanu.
Mmbuyomo, wachiwiri kwa sipikala a Madalitso Kazombo nawo adagamula pungu wakummwera kwa boma la Salima a Christopher Manja ndi phungu wa ku mmawa kwa boma la Rumphi a Kamlepo Kalua kuti asatenge nawo gawo pa zokambirana kwa masiku 5.
Awanso ankafuna kumenyana m’Nyumba ya Malamulo atasemphana pa nkhani yoti a Kalua adanyoza kuti palibe chomwe boma la Tonse Alliance likupanga komanso adaonjeza kuti boma silitenga chigawo cha kumpoto ngati chigawo cha m’Malawi.
“Palibe chomwe boma lapanga kumpoto mwina amaona ngati chigawo chakumpoto si Malawi. Zitukuko zonse amazipititsa pachigawo chapakati basi,” adatero a Kalua.
Koma mikangano yonseyo idayamba nyumbayo itangoyamba kumene kukumana pomwe atsogoleri a chipani cha DPP amakanganirana utsogoleri wambali yotsutsa boma.
Chipani cha DPP chidachotsa a Kondwani Nankhumwa pampandowo n’kuikapo a George Chaponda koma kaamba ka chiletso chomwe a Nankhumwa adatenga kukhoti, a sipikala adaletsa a Chaponda kulowa mumkumano wokonza za zokambirana m’nyumbayo.
Patsiku loti mtsogoleri wambali yotsutsa boma ayankhe uthenga wa a Pulezidenti wotsegulira zokambirana, anthu awiri a Nankhumwa ndi a Mary Navicha adaima nthawi imodzi kuti ayankhe mmalo mwa mbaliyo.
Izi zidayambitsa mkangano mpaka a sipikala adagwiritsa ntchito gawo 105 n’kuwauza a Navicha ndi aphungu ena omwe adali mbali yawo kuti asatenge gawo pazokambirana kwa masiku awiri.
Koma mtsogoleri wa Nyumba ya Malamulo a Richard Chimwendo Banda adadzudzula zomwe zimachitika m’nyumbayo ponena kuti aphungu amaiwala kuti amapita ku Nyumba ya Malamulo kukatumikira anthu.
Iwo adati n’zomvetsa chisoni komanso n’zokaikitsa kuti anthu angatume aphungu kupita ku Nyumba ya Malamulo kukawayimilira pandewu mmalo mokamba zachitukuko.