Nkhani

APM adzudzula Chakwera

Kadaulo pa ndale a George Phiri wati akugwirizana ndi zimene adanena mtsogoleri wakale wa dziko lino a Peter Mutharika kuti mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ayenera kuthana ndi mavuto omwe Amalawi akukumana nawo mmalo momanga otsatira chipani chawo cha DPP.

Koma kadaulo winanso a Ernest Thindwa wati a Mutharika ayenera kuzindikira kuti ndi bwalo la milandu lokha limene linganene ngati munthu ndi wolakwa kapena ayi.

A Mutharika: Musalimbane ndi ife. | Kondwani Kamiyala

A Mutharika, omwe adzaimire chipani cha DPP pa Chisankho Chachikulu pa 16 September 2025, adachititsa misonkhano yoimaima mu mzinda wa Blantyre pomwe adaima ku Mbayani, Che Mussa, Kameza, Lwanda, Khama, Makheta, Bangwe, Manje ndi Ndirande. M’malo onse amene amaima, a Mutharika adati a Chakwera kuti athane ndi mavuto a kusowa kwa mafuta, mankhwala m’zipatala, kukwera mitengo kwa zinthu, njala ndi mavuto ena ambiri.

Iwo adauzanso khamu la anthulo kuti A Chakwera aleke kumanga akuluakulu a chipanicho kaamba ka ndale. M’sabata ikuthayi, boma lidamanga wachiwiri wa DPP m’chipani cha kummwera a Joseph Mwanamvekha, phungu wa kummwera cha kummwera kwa Blantyre a Sameer Suleman ndipo padali chikalata choti apolisi akusaka a Norman Chisale, mkulu wa achinyamata m’chipanicho. A Chsale adakana kukadzipereka okha ku polisi momwe adachitira a Suleman.

Boma lidamanganso akuluakulu ena a boma a Lloyd Muhara, a Collins Magalasi, a Cliff Chiunda ndi a Jimmy Grey Kusamale, omwe adali mmodzi mwa akuluakulu a Greenbelt Authority (GBA).

“Lekani kumanga otsatira chipani cha DPP. Limbikirani kuthana ndi mavuto amene tikukumana nawo ngati dziko. Ndikupempheni Amalawi kuti ife tikubwerera m’boma pa chisankho chikudzachi choncho mudzativotere,” adatero a Mutharika.

A Phiri adati zimene adanena a Mutharikazo ndi zomveka, poonjezera kuti ndi udindo wa mtsogoleri aliyense kuthetsa mavuto omwe anthu ake akukumana nawo. Iwo ati boma la a Chakwera lakanika kuthana ndi mavuto a za chuma amene dziko lino likukumana nawo.

“Mukumbukire Kamuzu adanenapo kuti dzikola Malawi lili ndi adani atatu omwe ndi njala, nthenda komanso nsanje. Ndi udindo wa mtsogoleri aliyense kuti akonde anthu ake ndi kuonetsetsa kuti anthu a m’dziko la Malawi sakukumana ndi mavuto onga amenewa,” atero a Phiri.

Ndipo pa zomwe a Chakwera akuyenera kuchita, a Phiri ati palibe chomwe akuona kuti angawauzenso popeza ndi wosamva. Takhala tikukamba za ma mega farm kuti akambe kuti akolola mbewu zochuluka bwanji pakutha pa zaka zisanuzi koma mpaka pano sakambabe. Kodi ku mega farm akulimako zitsulo chani? Mbewu zosiyanasiyana monga nyemba ndi chimanga zimacha pasanathe ndi chaka n’komwe. Chomvetsa chisoni kuti kufika pano anduna a za ulimi sanayankhulepo pankhani ya mmene minda yaikuluyi adakololera,” atero a Phiri.

M’mawu awo, a Thindwa adadzudzula a Mutharika polankhulapo za milandu imene ili m’bwalo ponena kuti ndi khoti lokha lomwe limagamula ngati woganiziridwa ndi wolakwa kapena ayi choncho a Mutharika aleke kulowetsa ndale pa kumangidwa kwa mamembala a chipani cha DPP poti munthu aliyense atha kumangidwa.

“Tikuyenera kulemekeze malamulo a dziko lino ndiponso chigamulo cha khoti. Ngati munthu wapezeka wolakwa ndi bwalo la milandu akuyenera kumangidwa posatengera kuti uyu ndi wa chipani kapena uyu wangokhala nzika ya dziko la Malawi. Malamulo amagwira ntchito pa munthu aliyense,” adatero iwo.

Iwo ati pomwe dziko lino lili pa njala, n’koyenera kuti amene ali mu njala adziwike ndi kuthandizidwa. Iwo ayamikira boma pogawa chimanga kwa Amalawi omwe akhudzidwa ndi njala

“Onse amene ali pa chiopsezo cha njala ayenera kudziwika kuti boma lithenso kuthandiza anthuwo ndi njira zoepzera zakudya pofuna kuthetsa mavuto a njalayo,” atero iwo.

Poyankhapo, mneneri wa MCP mayi Jessie Kabwila ati a Mutharika apite ku polisi osati kumanena pa msonkhano wa chipani za nkhaniyi popeza chipani cha MCP sichimanga munthu koma apolisi ndiwo amamanga oganiziridwa kulakwitsa.

“Ndipemphe a Mutharikakuti aike chidwi chawo kumanga chipani cha anthu oti alibe mabelo m’manja. M’chipani mwawo mwangodzadza anyamata a mabelo m’manja, ngati akufuna mayankho pa nkhani ya kumangidwa kwa anthuwo apite kupolisi chifukwa apolisi amamanga munthu yekhayo amene walakwitsa, asamanamize anthu kumati chipani cha MCP ndi chomwe chikumanga anthu,” atero a Kabwila.

Polankhula kwa Luwanda m’taunishipi ya Machinjiri, Mwanamvekha omwe boma lidawamanga powaganizira kuti ndi a Muhara, a Magalasi, a Chiunda ndi a Kusamale adasokoneza K447.5 biliyoni ku kampani ya Salima Sugar yomwe ili pansi pa nthambi ya boma ya GBA adaseleula kuti ngakhale akuyankhula kwa anthuwo adakali mkaidi

“Ndikulankhula pano ndine mkaidi ndipo belo ili m’thumbamu,” adatero iwo.

Ndipo a Suleman, omwe adawamanga powaganizira kuti adalakwa ponena kuti akuluakulu ena a chipani cha MCP amawakonzera upandu, adati: “Ngakhale mukutimanga, kaya mutipha koma ife sitiopa. Chomwe Amalawi akufuna kuti mafuta azipezeka, zinthu zileke kukwera mtengo ndipo chakudya ndi mankhwala zizipezeka.”

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button