Nkhani

Akuluakulu 6 amangidwa m’masiku awiri

Akuluakulu omwe akudzimva fungo la milandu akuyenera kuyenda cheucheu kaamba koti unyolo wathyola mpanda ku polisi ndipo ukuika manja kumbuyo akuluakulu omwe akuwaganizira kusokoneza.

Lolemba ndi Lachiwiri sabata yomwe ikuthayi, akuluakulu 6 adanjatidwa ndipo ngakhale ena adapatsidwa belo ya khothi, milandu yawo ikupitirira malinga n’kuti ina aisuntha kuchoka ku khoti laling’ono kupita ku khoti lalikulu.

A Suleman: Adakadzipereka | Nation

Lolemba, unyolowo udagwera nduna yakale ya za chuma a Joseph Mwanamveka, yemwe adali mlangizi wa a pulezidenti pa zachuma a Collins Magalasi, mlembi wamkulu wa boma wakale a Lloyd Muhara, mlembi wamkulu wakale ku unduna wa za chuma a Cliff Chiunda ndi mlembi wakale wa nthambi ya Green Belt Authority (GBA) a Grey Kasamale.

Asanuwa akuwaganizira kuti adasowetsa K447.5 biliyoni ya boma kudzera ku kampani ya Salima Sugar Company pomwe adali m’maudindowo nthawi ya ulamuliro wa chipani cha DPP.

Kalondolondo wa m’chaka cha 2023 wa momwe chuma cha Salima Sugar chidayendera ndiye adafukula zoola zonse ndipo apolisi adagwiritsa ntchito lipoti la kalondolondoyo pomanga akuluakuluwo.

Mneneri wa polisi a Peter Kalaya ndiwo adatsimikiza za milanduyo komanso kumangidwa kwa akuluakuluwo.

Iwo adaonjeza kuti akuluakulu asanuwo, apolisi akusakasaka yemwe adali mkulu wa kampaniyo a Henri Njoloma omwe apolisi akuti akuthawathawa mlandu womwewu.

Kampani ya Salima Sugar Company Limited idatsegulidwa m’chaka cha 2015 pa mgwirizano wa boma ndi kampani ina yaku India yotchedwa AUM Sugar and Allied Limited pomwe boma lidali ndi masheya 40 pa 100 alionse ndipo kampani ya ku India idali ndi masheya 60 pa 100 alionse.

Kalondolondo wa 2023 yemweyo adavumbulutsanso kuti akuluakulu ena a kampani ya AUM Sugar and Allied Limited adakhudzidwa ndi mchitidwe wozembetsa ndi kutulutsa ndalama m’dziko muno zomwe zidapangitsa kuti mmodzi mw iwo a Shirieesh Betgiri omwe adali wapampando wa kampaniyo amangidwe.

Lolemba lomwelo, phungu wa dera la kummwera cha kummawa kwa mzinda wa Blantyre a Sameer Suleman a chipani cha DPP adakadzipereka m’manja mwa apolisi atauzidwa kuti pali walanti yowamangira.

Iwowa ali pa belo ya khoti ndipo akuwaimba mlandu wonyoza akuluakulu ena a m’boma kudzera patsamba la mchezo la chipanicho koma iwo atatuluka pa belo ya khoti adachenjeza apolisi kuti azisamala pogwira ntchito yawo kupangira pamawa boma litasintha.

“Ndikufuna kuuza anzathu apolisi kuti zina muzikana mukamatumidwa ndi anthu omwe ali m’boma pano chifukwa bomali lapita kale ndipo mawa lino m’mipando imeneyo tidzakhalamo ndife,” adatero a Suleman.

Ndipo mneneri wa chipani cha DPP a Shadreck Namalomba ati iwo akuona kuti boma likugwiritsa ntchito unyolo pofuna kukhazika chete otsutsa bomalo koma iwo ati otsutsa salola kuopsezedwa kwa mtundu uliwonse.

“Akufuna kuti otsutsa tizinjenjemera chifukwa adziwa kuti anthu ataya nawo chikhulupiriro ndiye akuona ngati kuopseza kukhoza kuwathandiza koma ife sitibwerera mmbuyo,” adatero a Namalomba.

Zonsezi zikuchitika pomwe dziko la Malawi likuyandikira ku Chisankho Chachikulu mwezi wa September chaka chino ndipo akuluakulu omwe amangidwawo ndi achipani chachikulu chotsutsa cha DPP.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button