Nkhani

Apolisi aphunzira kagwiridwe ka ntchito yawo

Listen to this article

Polisi ya Nkhotakota yakhala yoyamba kuphunzitsidwa za momwe angagwirire ntchito yawo panthawi ya zipolowe komanso zionetsero.

Maphunzirowa akudza poyang’anira chisankho cha pulezidenti, makhansala ndi aphungu a ku Nyumba ya Malamulo cha chaka chamawa.

Panthawiyi pamakhala zingapo zotsamwitsa mwina anthu kunyanduka posagwirizana ndi zotsatira zomwe zatuluka kapena kusamvetsetsa ndi momwe zina zachitikira.

Apolisi ndiwo amakhala kalikiliki kukhazikitsa bata kuti pasakhale zipolowe koma zonse zithere mokomera mbali zonse motsatira chilungamo.

Malinga ndi mneneri wa polisiyo, Kaitano Lubrino, ganizolo lidabwera ndi mkulu wa apolisi m’dziko muno Loti Dzonzi.

“Cholinga n’chakuti apolisi onse m’dziko muno aphunzitsidwe za momwe angachitire panthawi ya ziwawa pomwe anthu akufuna kuchita zionetsero.

“Polisi yathu yakhala ya mwayi kuti ndiyo yayamba kuphunzitsidwa za maphunzirowa. Maphunzirowa adachitika Lachinayi pa June 4,” adatero Lubrino.

Apolisi 40 adachita nawo maphunzirowo omwe mwazina amaphunzira za momwe angagwiritsire zida zawo ndi nthawi yake yomwe angagwiritsire zidazo.

Related Articles

Back to top button