Apolisi athotha gulu la MYP
Asilikali 56 a gulu la chitetezo la mtsogoleri wakale, Hastings Kamuzu Banda la Malawi Young Pioneer (MYP) ali zungulizunguli mu mzinda wa Lilongwe kusowa pokhala apolisi atawathamangitsa pa msasa wawo.
Mtsogoleri wawo, Franco Chilemba watsimikiza kuti apolisi adatulukira pa msasawo usiku wa Lachitatu n’kuyamba kuwathamangitsa.
“Adatiuza kuti tisadzabwererenso pamalopo,” adatsimikiza Chilemba.
“Tidangowona apolisi afika usiku. Poyamba tidamva kukuwa kwa anzathu omwe adayambirira kuwona apolisiwo. Kenako tonse titadzuka, tidangowona nantindi wa apolisi atazungulira msasa uku ena atalowa mu msasawo nkumathamangitsa anthu.”
Iye adati padali pikitipikiti pa msasawo usikuwo poti anthuwo adali asadakonzeke ndipo ena adayiwala katundu wina.
“Panopa anthu ali khumakhuma kusowa pokhala, ndi chakudya,” adatero Chilemba Lachinayi.
Mneneri wapolisi James Kadadzera adatsimikiza kuti ntchito yothamangitsa anthu pa msasawo idachitikadi koma adati lamulo silidachoke ku polisi koma ku khonsolo ya mzinda wa Lilongwe.
“Adali a khonsolo amene adagwiritsira ntchito apolisi kuti ntchitoyo itheke mosavuta,” adatero Kadadzera.
Mneneri wa khonsolo ya Lilongwe Tamara Chafunya samayankha lamya yake ya mmanja.
Gulu la MYP lidamanga msasa pafupi ndi chipilala cha chikumbutso cha Kamuzu ku Lilongwe mwezi wa July 2017 pofuna kukakamiza boma kuti lipereke ndalama zopumira pa ntchito kwa mamembala ake.
Gululo latha chaka ndi miyezi itatu pa msasawo ndipo posachedwapa boma lidayamba kulipira anthuwo kuti azipita kwawo koma Chilemba wati mamembala awo sakukhutira ndi ndalama zomwe akulandira.
“Panopa ayamba kulipira koma akupereka K500 000 kwa aliyese posatengera zaka zomwe munthu adagwirira ntchito ndiye mamembala sakukondwa nazo. Tonse tidalipo 159 ndipo 103 ndiwo alandira, 56 otsalawo sadalandire ndipo ndiwomwe athamangitsidwa pa msasapo,” adatero Chilemba.
Iye adati anthuwo salola kubwerera kwawo chimanjamanja chifukwa ataya kale nthawi yayitali pa msasapo ndipo alolera kuzunzidwa.