Nkhani

Ayamikira boma pa ganizo lotsegulanso sukulu

Listen to this article

Komiti yotsogolera kulimbana ndi matenda a Covid yalengeza kuti sukulu zonse zitsegulidwe Lolemba likudzali pa 22 February.

Nduna ya zaumoyo Khumbize Kandodo yemwe ndi mmodzi mwa a pampando a komitiyo wati kauniuni wasonyeza kuti mphepo zili bwino kuti sukulu zikhoza kutsegulidwa.

Adalengeza kutsegulira kwa sukulu: Chiponda

Akadaulo ayamikira ganizoli koma ati unduna wa za maphunziro ugwiritse bwino ntchito K5 biliyoni yomwe walandira kuchoka pa K17 biliyoni yomwe boma lapeeeka ku nkhondo yolimbana ndi matendawa.

Kadaulo pazamaphunziro Benedicto Kondowe wati kugwiritsa bwino K5 biliyoni polimbana ndi matrndawa, chitetezo chikhoza kukhwima m’sukulu.

Iye wati sipakufunikaso kuti zidzafikenso poti mpakana kutseka sukulu ndi phunziro lomwe dziko laphunzirapo paulendo woyamba ndi wachiwiri womwe.

“Zidzakhala zochititsa manyazi kuti sukulu zidzafikenso potseka, apapa ana asokonezeka kale kokwana kwinako ambiri adzangosiya sukulu. K5 biliyoni ikhoza kuthandiza kupewa zimenezo itagwira ntchito bwino,” adatero Kondowe.

Pulezidenti wa eni sukulu zoyima pazokha Joseph Patel adati sukulu zoima pa zokha zidakonzeka kalekale koma zimangodikira lamulo la boma kuti sukulu zitsegulidwe.

“Apapa zakhala bwino chifukwa ife a sukulu zoima pa zokha tidakonzeka kalekale potsatira zomwe boma lidati n’zofunika pasukulu m’nyengoyi,” adatero Patel.

Iye adati chifukwa china choyenera kutsegulira sukulu n’choti ana ndi aphunzitsi omwe adapezeka ndi Covid adachira ndiye chitetezo m’sukulu chidakwera.

Katswiri wina pa maphunziro Limbani Nsapato adati boma likhale ndi chidwi chachikulu pa chitetezo m’sukulu chifukwa matendawa akadzabukanso m’sukulu zidzaonetsa kulephera.

“Boma likhoza kukwanitsa kuteteza ana asukulu ndi aphunzitsi awo ku Covid ndiye sitikuyembekezera kuti tidzamvenso zoti matendawa abuka m’sukulu,” adatero Nsapato.

Pulezidenti Lazarus Chakwera adalamula kuti sukulu zitsekedwe kwa sabata zitatu pa 17 January 2021 m’sukulu zina monga Lilongwe Girls mutabuka matendawa.

Sukuluzo zimayenera kutsegulidwa pa 8 February 2021 koma Chakwera adaonjezera sabata zina ziwiri kuti aonererebe chifukwa n’kuti nthawiyo matendawo atafika pa indeinde.

Aka kadali kachiwiri kutseka sukulu chifukwa cha Covid. Chaka chatha, sukulu zidatsekedwanso kwa miyezi 5 ndipo pomalizira pake asungwana ambiri adapezeka ndi pathupi ndipo ena adakalowa kumabanja.

Related Articles

Back to top button