Nkhani

Aphungu akumana lolemba

Listen to this article

Aphungu a Nyumba ya Malamulo ayamba kuunika momwe bajeti ya 2020 mpaka chaka chino yayendera m’miyezi 6 yoyamba Lolemba likudzali kuti aunikire moyenera kusintha ndi kuwongola.

Akadaulo pa nkhani zosiyanasiyana ati aphunguwo aonetsetse kuti mkumanowo waika mtima poongola dziko pa zinthu zingapo zomwe zidaima kapena kubwerera mmbuyo.

Aphungu ayamba mkumano Lolemba

Nyumbayo yalemba patsamba lake la Facebook kuti mkumanowo uyamba Lolemba pa 22 February 2021 ndipo udzatha pa 26 March 2021.

“Mkumanowo udzayenda m’njira ziwiri nthawi imodzi popewa kufalitsa Covid. Aphungu ena azidzakhala m’nyumbamo pomwe ena azidzatsatira pa Intaneti koma onse akuyenera kudzakhala mumzinda wa Lilongwe nthawi yonse,” yatero komiti yokonza ndondomeko ya zokambirana m’nyumbayo.

Matenda a Covid adayambanso kuvuta kumapeto kwa mwezi wa December 2020 bajeti ya 2020/2021 yomwe inkapangidwa matendawa atapola moto itadutsa kale ndipo akadaulo adati asakhale chifukwa cholepheretsa mkumanowo.

Akadaulowo amayankha Tamvani potsatira malipoti awiri otsutsana oti nyumbayo siyitsegulidwa chifukwa cha Covid pomwe lina limati aphungu akumana pogwiritsa ntchito njira zosafalitsa Covid.

Kadaulo pazaumoyo George Jobe adati nyumbayo ilibe chisankho koma kukumana chifukwa ino ndiye nthawi yofunika aphunguwo kukambirana zamavuto omwe ali m’dziko muno.

“Akati kutumikira anthu n’kumeneku. Panopa dziko lili m’mavuto ambiri ofunika bajeti iunikidwenso kuti ikhale ndi njira zothanirana ndi mavutowo,” adatero Jobe.

M’dziko muno muli mavuto monga matenda a Covid, maphunziro adaima, bizinesi sizikuyenda komanso pali mphekesera zoti ndalama zina zothsna ndi Covid sizidayende m’chilungamo.

Mkulu wa bungwe la Center for Democracy and Economic Development Initiative (Cdedi) Silvestre Namiwa adati ngati komiti yoona za kasankhidwe ka adindo m’boma idakwanitsa kukumana pa nkhani ya makomishona awiri a MEC ndiye kuti pali kuthekera koti nyumbayo ikhoza kutsegulidwa.

“Akumane chifukwa pali mafunso ambiri omwe mayankho ake angachokere muzokambirana za aphungu. Pali nkhani zambiri zoti kuyamba kutambasula pano mpakana dzuwa kulowa. Apeze njira yokumanirana kaya pamaso mpamaso kaya pamakina koma akambirane,” watero Namiwa.

Cholinga cha mkumanowu chimakhala kuunika momwe bajeti yayendera pa theka lachaka ndi kusintha moyenera kusinthidwa malingana ndi momwe nyengo ikuonekera.

Kadaulo pa zamaphunziro Limbani Nsapato wati nzachidziwikile kuti bajeti ikuyenera kusintha kuti unduna wa za maphunziro ulandire ndalama zokwanira zolimbana ndi Covid uku sukulu zikuyenda.

“Ophunzira akuyenera kuganiziridwa, n’zachidziwikite kuti apapa bajeti ya za maphinziro ikuyenera kukwera kuti sukulu zitsegulidwe ndiye aphungu akungoyenera kukumana,” watero Nsapato.

Nkhani ina yomwe anthu akuyidandaula pankhondo yolimbana ndi matendawa ndi mchitidwe wa apolisi ena omwe akuti akumenya anthu mwa nkhanza ndipo ena akutengera mphamvu katundu makamaka mmalo ogulitsira mowa akadutsa nthawi yotseka.

Mkulu wa gulu lomenyera anthu ufulu la HRDC Gift Trapence wati aphungu asalephere kukumana ndipo nkhani ya chitetezo makamaka polimbikitsa anthu kutsatira njira zopewera Covid ikakambidwe.

“Apapa akumane ndipo akambirane za malamulo omwe adakhazikitsidwa polimbana ndi Covid ndi kuunikira momwe apolisi ikuyenera angagwilire ntchito yawo,” adatero Trapence.

Nyumbayo inkayenera kutsegulidwa pa 8 February 2021 mpaka pa 15 March 2021 koma zidakanika chifukwa nyengoyo idali yomwe matenda a Covid amafala kwambiri mpaka kupha aphungu ena.

Komitiyo yati pambali pounika momwe bajeti yayendera pa theka la chaka, adzakambirananso bilu yakayendetsedwe ka chuma, bilu yakuima pa yokha kwa Nyumba ya Malamulo ndi malipoti a makomiti.

Related Articles

Back to top button
Translate »