Banja lituluka pa belo
Bwalo la milandu mu mzinda wa Blantyre, Lachisanu lidapereka belo kwa mayi Linda Chitala ndi amuna awo a Macferson Chitala amene akuyankha mlandu woti amazunza mwana wawo wa zaka 4.
Apolisi ya South Lunzu ku Machinjiri mu mzindawo adamanga awiriwo mu December chaka chatha, oyandikana nawo nyumba atakamang’ala ku polisi kuti mayiwo amazunza mwana wawo womupeza. Zithunzi za mwana wa mkaziyo ali ndi zilonda thupi lake lonse komanso tsitsi litakudzuka zidafala m’masamba a mchezo.

Bwalo la milandulo likuzenga a Linda mlandu wovulaza mwana kwambiri mwadaladala mosemphana ndi gawo 235 (a) la malamulo a zilango m’dziko lino ndipo chilango chachikulu kwambiri atawapeza wolakwa n’kukakhala ku ndende moyo wawo onse.
Ndipo awiriwo akuwazenga milandu ina iwiri limodzi. Woyamba ndi wosemphana ndi gawo 165 la zilango limene limati kholo kapena a Vitumbiko Mbizi omwe ndi loya wa bungwe la maloya a chizimayi adapempha woweruza kuti apereke chigamulo chokhwima kuti ena atengerepo phunziro. “Ngati wapolisi, iwowatu anali ndi udindo waukulu woteteza mtsikanayu, osati kumugwiririra,” atero iwo.
Ndipo woweruza a Martin Chipofya ati chifukwa cha kukula kwa mlanduwo autumiza ku bwalo lalikulu la High Court, kuti likapereke chigamulo choyenera. “Podikilira chigamulocho akhalabe ali mu ndende,” atero iwo.