Ati tikhwimire mwana
Ndili pa banja ndipo tili ndi ana angapo. Banja lathu ndi loopa Mulungu. Ndipo tonse ndi atsogoleri ku mpingo wathu.
Ndakhala ndi kumadabwa ndi amuna anga zochitika zawo makamaka tikakhala ku nyumba. Chikhristu chathu chimaonekera ku mpingo kwathuko koma ngati tili ku nyumba amuna anga amachita zinthu zosiyana ndi mmene alili.
Akhala akundifunsa kuti kodi sufuna titalemera kwambiri? Ine funso limenenli limandidabwitsa zedi.
Chifukwa ifeyo si osauka. Chilichonse tili nacho ndipo sitisowa kanthu. Anthu ambiri amatinena kuti ndife ochita bwino. Ana athu amapita m’sukulu zapamwamba.
Amuna anga andiuza kuti akufuna akhwimire mwana wathu mmodzi. Akuti tilemera kwambiri.
Anatche, ine zimenezi zandidwalitsa kwambiri. Ndipo ndapezeka kuti ndili m’chipatala. BP yanga idakwera kwambiri.
Koma pano yatsikirapo, ndipo ndayamba kumva bwino.
Ndilibe chikhumbokhumbo chopitanso ku nyumba kwanga. Chomwe ndikufuna ndi kukhala pamodzi ndi ana anga basi. Ndikungokhala ndi mantha kuti andiphera ana abambo amenewa. Akabwera kudzandiona ndikungokhala wa mantha basi. Sindikudziwa chomwe akufuna. Nanga chuma tili nacho chambiri ndiye chofunira kukhwima ndi chiyani?
Maganizo anga ndi oti ndikatuluka kuno ndikafikire kwa abale anga. N’kapeza bwino ndipite ku khoti ndikathetse ukwati. Ndili ndikuthekela koti ndingathe kusamala anawa pa ndekha.
Ndithandizeni Anatche.
JCT
Mwana wanga ndati ndikuuze kuti si onse amene amapemphera omwe ali olungama.
Kupemphera kwa anthu ambiri ndi kwachipha maso basi. Amuna anu kupemphera kwawo ndi kongovala ngati zovala. Iwowa amaphimba zambiri ndi kupemphera kwawo. Ndipo kulimbikira ku tchalichiku n’kofuna kuti abise mawanga awo.
Chomwe ndingakulangizeni n’choti mupemphere kwambiri kuti zomwe akufunazo zisatheke.
Ngati mungathe, pemphani ena akuthandizeni kupemphera. Mupemphere modzikhutula kwambiri kuti Ambuye akuthandizeni nkhondo imeneyi. Pemphero ndiye chida chokutetezerani ku mavuto onga amenewa.
Tithokoze kuti akuuzani zomwe akufuna kupanga. Alipo amuna ena sanenena, iwe umangodabwa kuti ana akutha.
Khalani nawo pansi bwinobwino ndi kuwalongosolera kuti zomwe akufunazo ndizosayenera pamaso pa Mulungu. Muwauze motsindika kuti inu simukufuna kukhetsa mwazi (kapena kuti simungaphe mwana wanu.) Mulungu zimenezo sakondwera nazo. Chuma chokhetsela mwazi sichimakhalitsa.
Ngati angalimbikire, thetsani banjalo ndi kutenga ana anu. Komanso mudzawatsimikizire kuti mwana aliyense atati afe mukawasumira.