Nkhani

‘Boma litisamale pa nkhani ya malo’

Listen to this article

Alimi ena ang’onoang’ono m’maboma a Mulanje komanso Thyolo achenjeza boma kuti lisanyozere madandaulo awo akusowa kwa malo ponena kuti maesiteti ambiri akupitilira kuphangira malo m’maboma awiriwo.

Mwa zina, anthuwo—omwe alipo osachepera 200 000—akuti akusowa pokhala, ngakhale polima kaamba kakuchulukana kwa chiwerengero cha anthu m’maderawo, chomwe chakwera m’zaka zadutsazo.

Alimi a m’boma la Thyolo kuchita ziwonetsero zosakondwa ndi kuphangira kwa malo a maesiteti a tiyi posachedwapa

Izi akuti zikuchitika pomwe kampani zolima tiyi m’maderamo zimangosunga malo ena ambiri omwe sizigwiritsa ntchito.

Mtsogoleri wa gulu loyimira anthu odandaulawo la Concerned Landless Citizens of Thyolo and Mulanje Harry Mikuwa adauza Msangulutso kuti umphawi komanso njala za mgonagona zikhoza kuyala mphasa m’mabomawo kaamba kakuti tsopano anthu ambiri afika posoweratu malo olima, ngakhalenso okhala.

Komabe iye adatsindika kuti bungwe lawo liri ndi chikhulupiliro chokhazikika mu boma la Tonse, ati poyerekeza ndi maulamuliro ena a mmbuyowo, omwe iye adati ankangoitenga nkhaniyo ngati chida chokwelera pa ndale.

Mikuwa adafotokoza: “Izi zisalowenso ndale. Tatopa nazo tsopano. Pano tikufuna boma litithandize kuunikanso mapangano omwe kampanizo zidapanga ndi dziko lino chifukwa uku n’kudyerana masuku pamutu. Sizoonayi kuti lizi ya malo, kapena kuti kubwereka kungachite kupyolera zaka 100. Atipatse malo omwe akungosungawo—omwe ndi zachidziwikire kuti ndi amakolo athu—tidzilima komanso kukhalapo.

Iye adachenjeza boma likachita chibwana pa nkhaniyi, mavuto omwe akudza kaamba ka vuto la malowo, adzagwera dziko lonse.

“Zaka zikupita ndipo ana aja akukula. Ndi kuvuta kwa maphunziro mdera lino, aboma ndi aliyense wakufuna kwabwino adzifunse kuti ndi Malawi wotani yemwe tikumanga mwa ana oterewa?“ mkuluyo adatero.

Polankhula ndi Msangulutso, nduna ya za malo Kezzi Msukwa adatsimikiza kuti adalandiradi madandaulo a alimiwo, ndipo kuti unduna wake uli ndi chidwi chofuna kuthandizapo pa nkhaniyo.

Mwa zina, Msukwa adati adapita kale kukayendera zina mwa kampani za minda ya tiyi m’mabomawo pofuna kumva mbali zonse pankhaniyo boma lisadapange chiganizo chokhazikika.

“Nkhaniyo ndi yoona ndipo ndivomere pano kuti mpofunikadi kuiunikira bwino lomwe. Komanso tikupempha mbali zonse ziwiri kuti zikhale ndi bata. Zachipolowe zomwe zikumamvekazi sizikutipatsa fungo labwino ngati Amalawi. Tikapanda kusamala, tipezeka kuti tikutemana tokhatokha pa nkhani yomweyo; zomwe zingakhale zodandaulitsa.

Padakali pano, a Msukwa adatsindikanso kuti boma likutenga ganizo la zokambirana ngati loyenera pofuna kubweretsa kumvana pa nkhaniyo.

“Tidakumana nalo kale gulu la odandaulalo ndipo tikukonzanso msonkhano wa onse okhudzidwa, kuphatikizapo mafumu, a zachitetezo komanso eni ma esteti kuti tidzamvane chimodzi. Tikakonzeka, tikuuzani,” ndunayo idatero.

Koma polankhulapo, mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Centre for Democracy and Economic Development Initiatives (Cdedi) Silvester Namiwa adaikira kumbuyo alimiwo, ponena kuti apusitsidwa kokwanira pa nkhaniyo.

“Ulendo uno, tikufuna tiliuze boma kuti Malawi sakuphethiranso. Ngati boma ili lili lotsimikizika pa ntchito yotukula anthu mdziko muno, likungoyenera kukhala tcheru pa nkhani ya malo chifukwa umenewu ndi mgodi wa nzika za dziko lino.

“Nzika ikamasowa pokhala, polima, dziwani kuti boma limenelo ndi lolephera. Mizimu ya anthu a ku Thyolo komanso Mulanje idzakhala pansi aliyense akadzayamba kudya kuchokera mmunda mwake,” adatero Namiwa.

Bungwe la Cdedi lidalemberapo kalata ku dziko la Britain pofuna kulikakamiza kuti lipereke chipukuta misozi kwa mabanja a m’mabomawo ati ponena kuti dzikolo lidalanda mwa nkhanza malo ambiri omwe muli kampani za tiyi, ndi kutinso ena adataya miyoyo.

Adafotokoza Namiwa: “Nkhawa yathu imakhala pa amai ndi ana. Mukaonetsetsa, ma banja ambiri mmadera tatchulawo amakhala opanda bambo pakhomo ndipo mmalo mwake, ana ndi amene amakakamizika kukasaka zapakhomopo. Izi ndi zomwe zikulepheretsa ana maphunziro chifukwa cha kutenga mimba zosayembekezeka komanso kulowa m’banja adakali aang’ono. Chipukuta misozi chomwe tinkapempha chinkaunikira zonsezo.”

Chifukwa chosowa pogwira, anthu ambiri m’maboma a Thyolo komanso Mulanje amadalira kugwira maganyu m’minda ya tiyi, momwenso malipiro ake sakhala olozeka.

Related Articles

Back to top button
Translate »