Chisankho chipitirire—bwalo
….Khoti lalikulu likana pempho la MEC
Bwalo lalikulu la milandu la Supreme Court Lachinayi lidakana pempho la bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) kuti zokonzekera chisankho ziimikidwe kaye mpaka mlandu omwe bungwelo likuchita apilo kuti bwalo la Constitutional Court silidagamule bwino.
Mwa zina, woimira MEC Tamando Chokotho adauza oweruza 7 kuti MEC imafuna kuti zokonzekera chisankho ziimikidwe chifukwa bungwelo lidali ndi nthawi yochepa kuti likonzekere. Constitutional Court idalamula pa 3 February kuti chisankho cha pa 21 May 2019 sichidayende bwino ndipo chisankho china chichitike pasanathe masiku 150.
Koma malinga ndi Chikosa Silungwe yemwe ndi woimira wodandaula woyamba mtsogoleri wa UTM Party Saulos Chilima adati majajiwo palibe adaonapo pa mfundo za MEC.
Izi zikutanthauza kuti MEC iyenera kupitiriza zokonzekera chisankho chimene aphungu adati chidzakhalepo pa 19 May chaka chino.
Bwalo la Supreme pa 15 April lidzayamba kumva nkhani imene MEC komanso mtsogoleri wa dziko lino adakamang’ala kukhoti kuti chigamulo choti sichidayende bwino achitaye.
Padakalipano, MEC yalemba maloya a ku South Africa kuti adzaimire bungwelo ndipo adzawalipira K600 miliyoni. Koma unduna wa zachuma wati sukudziwapo kanthu pankhaniyi imene akadaulo ena ati n’kuononga chuma cha boma.
Izi zili apo, khumbo la Amalawi ena loti mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika asadikire masiku 21 omwe malamulo amam’patsa kuti asayinire mabilu omwe aphungu a Nyumba ya Malamulo avomereza ladzutsa mavu m’khomola.
Mutharika akuyenera kusaina mabilu okhudza momwe chisankho chobwereza cha Pulezidenti chiyendere ndipo pa masiku 21 omwe adali nawo, iye watsala ndi 5 koma malingaliro a Amalawi ena kuphatikizapo HRDC adali oti Mutharika asadikire masiku 21.
Malingalirowo amachokera pa nkhawa yoti chisankho chomwe chikuyenera kuchitika pa 19 May 2020 chikudikira mabiluwo ndiye kuchedwetsa kusainira mabiluwo kukhoza kusokoneza zokonzekera za chisankhocho.
Pofuna kukakamiza Mutharika kusaina mabiluwo msanga, HRDC idalengeza pamsonkhano wa atolankhani pa 6 March 2020 kuti idzatsogolera Amalawi kukatseka nyumba za boma za Kamuzu Palace, Chikoko Bay ndi Mzuzu State Lodge pa 25 March 2020.
Potsatira chikonzerocho, apolisi adamanga atsogoleri atatu a HRDC omwe ndi Timothy Mtambo, Gift Trapence ndi MacDonald Sembereka powaganizira kuti adaphwanya magawo 103, ndi 124 amalamulo adziko lino. Kumangidwako kudadza Mutharika atanena pamsonkhano kuti apolisi ayenera kugwiritsa mphamvu zawo kuti zionetserozo zisachitike.
“Gawo 103 la malamulo a polisi limaletsa munthu aliyense kapena gulu kukakumana kufupi ndi nyumba ya chifumu pa mamita ochepera 100 pomwe gawo 124 limaletsa munthu kutuntha anzake kuti aphwanye lamulo zomwe akuluakuluwa achita,” idatero kalata yapolisi.
Atatuwo adatulutsidwa pabelo Lachinayi ndipo bwalo lidagamula kuti apereke ndalama yokwana K200 000 ndipo azikaonekera kulikulu la apolisi ku Area 30 ku Lilongwe. Iwo adalangizidwanso kuti asasokoneze zofufuza za mlanduwo ndipo apereke shulite ya K2 miliyoni aliyense.
M’sabata ikuthayi, chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chidaimitsa kaye zionetsero zimene chidakonza kuchita Lachinayi pofuna kukakamiza apolisi kutulutsa atatuwo.
Koma kadaulo pa zamalamulo Prof Edge Kanyongolo adati pakadalipano, Mutharika sadaphwanye lamulo lililonse posasayina mabiluwo potengera malamulo.
“Gawo 73 la malamulo limapereka masiku 21 kwa Pulezidenti kuti asayine bilu ndiye panopo masikuwo sadakwane komanso gawoli limati Pulezidenti ali ndi ufulu wobweza bilu yosasayina koma ndi zifukwa,” adatero Kanyongolo.
Iye adapitiriza kuti biluyo ikabwerera ku nyumba ya malamulo ndi zifukwazo, Gawo 73 (4) limapereka mphamvu ku Nyumba ya Malamulo kuunika zifukwazo n’kulibwenzanso kwa Pulezidenti kuti asayine.
“Zikafika pa ndime iyi, Pulezidenti sakhalanso ndi mwayi wosankha kusayina kapena ayi chifukwa gawoli limati Pulezidentiyo asayine pa masiku 21 basi ndipo akalephera apo, ndiye kuti tsopano waphwanya malamulo,” adatero Kanyongolo.
Koma mneneri wa Pulezidenti Mgeme Kalirani adati Mutharika sakuthamangira kusayinira mabiluwo chifukwa malamulo amam’patsa masiku 21 ndipo masikuwo sadakwane.
Pazokonzekera za chisankho chobwereza, mneneri wa Malawi Electoral Commission (MEC) Sangwani Mwafulirwa adati bungwelo lidzatulutsa ndondomeko ya zokonzekera zonse zikapsa.