Njovu ziwiri zitengetsana pa 19 May
Zadziwika tsopano kuti njovu ziwiri zomwe ndi mgwirizano wa Democratic Progressive Party (DPP) ndi United Democratic Front (UDF) komanso Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM Party ndizo zidzalimbane pachisankho cha pa 19 May.
Izi, zidatsimikizika Lachitatu zipani za MCP ndi UTM zitabwera poyera n’kunena kuti m’gwirizano wawo womwe wakhala mphekesera chabe kwa nthawi yaitali tsopano watheka.
Izi zikutanthauza kuti tsopano zipani zinayi zomwe zidali zikuluzikulu pachisankho cha pa 21 May chaka chatha tsopano zapanga mbali ziwiri zomwe zidzapikisane pachisankho chomwe chikubwerachi.
Zipani za DPP ndi UDF zidalengeza mgwirizano wawo pa 25 February pomwe MCP ndi UTM ati mgwirizano wawo wangopsa kumene ndipo adzasainira pa 19 March ku Bingu International Convention Centre (BICC) ku Lilongwe.
Polengeza mgwirizano wawo, DPP ndi UDF onse adati adaona kuti mfundo zawo zachitukuko ndi zolinga zawo n’zofanana ndipo MCP ndi UTM nawo akunena zomwezo.
Migwirizanoyi yapangidwa pokonzekera chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chobwereza potsatira chigamulo cha Constitutional Court choti chisankho cha pa 21 May sichidayende bwino ndipo chibwerezedwe.
Khothilo lidagamula kuti chisankhocho chichitike m’masiku 150 kuchokera pa 3 February 2020 pomwe lidapereka chigamulo chake chomwe chidakomera Lazarus Chakwera wa MCP ndi Saulos Chilima wa UTM Party.
Awiriwa adakamang’ala kukhoti kuti bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidapotoza zotsatira zachisankhocho chomwe lidapambanitsa Peter Mutharika wa DPP.
Koma zokonzekera chisankhocho ziyembekeza kuti mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika asainire mabilo a zachisankho amene aphungu a Nyumba ya Malamulo adapereka kwa iye.
Mwa zina, mabilowo akuti chisankho cha aphungu ndi makhansala chotsatira chidzachitike mu 2025 kuti chidzalingane ndi cha mtsogoleri wa dziko lino.
Aphunguwo adapemphanso Mutharika kuti achotse makomishona a MEC amene bwalo lidawapeza kuti sadayendetse bwino chisankho cha pa 21 May chaka chatha.
Oimira ufulu wa anthu Timothy Mtambo, Gift Trapence ndi MacDonald Sembereka adamangidwa pokonza zionetsero zokakamiza Mutharika kuchotsa makomishonawo.
Wotambasula za ndale Humphreys Mvula wati polingalira za nthawi yomwe yatsala kuti chisankho chichitike, n’koyenera kuti Pulezidenti asadikire masiku 21 kuti asayinire mabiluwo. “N’zoona malamulowo akutero koma apapa tikuyang’ana nthawi yomwe ilipo kuti chisankho chichitike,” adatero iye.