Kalembera wa zisankho ali mkati

Dzuwa salozerana, kalembera wa zisankho udayamba Lachiwiri m’maboma a Dedza, Salima ndi Kasungu.

Izitu zikudza pokonzekera chisankho cha makhansala, aphungu a Nyumba ya Malamulo ndi mtsogoleri wa dziko lino chomwe chidzachitike mu May chaka chamawa.

Ntchito ya kalembera m’boma la Salima

Aliyense ali ndi mwayi wodzavota akalembetsa. Kutanthauza kuti ngati munthu salembetsa, sadzapeza mwayi wodzaponya nawo mavoti.

Komishona wa bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC), Yahaya M’madi, wati ntchitoyo yayamba bwino moti akuyembekezera kuti sipakhala zotsamwitsa zina zilizonse.

“Majeneleta tabweretsa kuti magetsi akazima, ntchito isasokonekere. Zida zomwe tikugwiritsira ntchito ndi zamakono moti zikuthamangitsa kwambiri ntchito,” adatero M’madi.

Malinga ndi M’madi, anthu sazikhala pa nzere nthawi yaitali chifukwa makina omwe akugwiritsa ntchito ndi apamwamba.

“Mphindi ziwiri zokha munthu walembedwa kale, ndi zachangu,” watero mkuluyu.

Kalembelayu azichitika masiku 14 pa boma lililonse. M’boma la Dedza lokha, MEC ikuyembekezera kulembetsa anthu 400 000.

Share This Post