Nkhani

‘Kasanthuleni za chisankho’

Pamene aphungu a Nyumba ya Malamulo akukonzekera kukumana kuyambira Lolemba likudzali, akadaulo ena awapempha kuti akalunjike pa za chisankho cha 2019.

Ngakhale aphunguwo akhale akukambirana za momwe ndondomeko ya zachuma yayendera katswiri pa ndale George Phiri yemwe amaphunzitsa ku University of Livingstonia (Unilia) wati nkhani zina zonse zikhoza kuyamba zaima koma nkhani ya chisankho njofunika kuikambirana chifukwa ikukhudza tsogolo la dziko.

Aphungu m’Nyumba ya Malamulo mmbuyomu

Zipani za ndale zakhala zikuthirira ndemanga pa za kalembetsedwe konyentchera m’kaundula wachisankho, nkhani zokhudza zipolowe pa ndale, kusowa kwa makina akalembera ndi mphekesera zofuna kudzabera chisankho ndipo Phiri wati uwu ndi mpata woti aphungu akakambirane nkhanizi mwachindunji.

“Nkhani ya bajeti ili apo, aphungu asakataye nthawi ndi za ziii ngati momwe amachitira muja. Nthawi yatha, uwu ndi mwayi wawo wokonza Malawi. Kukonza Malawi ndi chisankho chomwe chikubwerachi,” adatero Phiri.

Iye adati n’kofunikanso kuti aphungu asanthule bwino za momwe akhala akuyendetsera thumba la ndalama za chitukuko la Constituency Development Fund (CDF). Ndemangayo ikudza pomwe lipoti ya nduna ya zachuma Goodall Gondwe kumayambiriro a chaka chino lidaonetsa kuti aphungu 20 adasokoneza ndalama za CDF koma mpaka lero palibe phungu amene adatchulidwa ndi kusololako.

“Phungu aliyense amalandira K18 miliyoni mu bajeti iliyonse koma apanga nayo chiyani cholozeka? Anthu akuvutikabe ngati kale,” watero Phiri.

Katswiri pa za kayendetsedwe ka dziko Makhumbo Munthali wati aphungu ayenera kukambirana za momwe chisankho chingayendere mwa bata ndi chilungamo. Iye adati pali nkhani zingapo zimene a zipani akhala akudandaula monga kalembera wa zisankho wophotchoka, kusowa kwa makina ku bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) zomwe zidadzetsa chikaiko zimene aphungu akuyenera kukaunikira.

“Pambali pokambirana mfundo zoti chisankho chidzakhale cha mtendere ndi chilungamo, akumbukirenso nkhani zina monga mabilu okhudza zachuma monga za migodi. Ndalama zankhaninkhani zikutuluka m’dziko muno chifukwa chopanda mfundo zokhwima,” watero Munthali.

Chipani cha People’s P(PP) chati chikugwirizana ndi maganizo a anthu ndi akadaulo pa nkhani zofunika ku nkhumano ya aphungu.

Mneneri wachipanichi Ackson Kalaile wati nkhani ya chisankho njosathawika pafikapa chifukwa ikukhudza miyoyo ya aMalawi.

“Tafika pano Amalawi adataya chikhulupiliro ndiye ntchito yonse yobwezeretsa chikhulupilirocho ili mmanja mwa aphungu ndipo nthawi yake ndiyomweyi, “ adatero Kalaile.

Mneneri wa Malawi Congress Party (MCP) Maurice Munthali adati akuluakulu achipanichi ndi aphungu ake akumana mawa Lamulungu kuomba mkota wa mfundo zopita nazo kunyumbayi.

Mneneri wachipani cha Democratic Progressive (DPP) Nicholas Daus adati chipanicho sichingakambe mfundo zake ndi atolankhani chifukwa zopita kunyumba yamalamulo zili ndi njira yake yodzera.

Iye adati zonse zikakonzeka, komiti yoyenera idzalengeza.  “Sitingamakambirane ndi atolankhani mfundo zomwe takambirana choncho ndilibe yankho, “ adatero Dausi

Posanthula nkhani ya momwe aphungu agwirira ntchito mmbuyomu, iye adayamika momwe aphunguwo adatsatira nkhani yomwe nduna yakale ya malimidwe George Chaponda amamuganizira kuti adachita chinyengo pogula chimanga kuchoka ku Zambia.

Iye adati ngakhale izi zili choncho, aphungu amene adasankhidwa mu 2014-wa akanika m’zambiri chifukwa mmalo mothandiza kutukula dziko, iwo adathandizira kulilowetsa pansi.

“Aphungu adayesetsa kukoka nkhaniyo ya chimanga ndipo tidayamika, koma tikawayika pasikelo ya udindo wawo, palibe chomwe adachitapo m’zaka zonsezi,” adatero Munthali

Amalawi ena amene tidacheza nawo aonetsa kuti khumbo lawo lagona poti aphungu akambirane zakupsa zokhudza chisankho.

Jane Mapira wa ku Lilongwe wati iye akadakonda aphungu akadakambirana nkhani yokhudza kusintha akuluakulu a MEC omwe wati akhumudwitsa kale anthu nzochitika zawo.

Wilson Thomas wa ku Zomba wati iye sakuona choti aphungu azikatayira nthawi n’kukambirana zinthu zomwe sizingasinthe kalikonse ndipo wati kuli bwino aphungu akangokambirana za bajeti n’kumabwerako.

“Ngakhale atakambirana nkhani za chisankho, palibe chingasinthe chifukwa nthawi yatha kale. Apa akangokambirana za bajeti n’kumabwerako kukadikira chipande mu May chaka cha mawachi basi,” watero Thomas.

Ukatha msonkhano wa aphungu wa chaka chino, aphunguwo adzaakumana komaliza mwezi wa March chaka cha mawa, kutangotsala miyezi iwiri kuti chisankho cha 2019 chichitike.

Related Articles

Back to top button