Nkhani

Anthu 6.9 miliyoni alembetsa mavoti

Listen to this article

Zotsatira za kalembera wa mavoti zomwe bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) latulutsa zasonyeza kuti anthu 6 856 295 ndiwo alembetsa m’dziko lonse kuti adzaponye nawo voti chaka cha mawa.

Bungwe la MEC limayembekezera kulemba anthu 8 510 625 m’maboma onse m’magawo onse 8 koma chifukwa cha zovuta zina zomwe bungweli limakumana nazo mkati mwa ndime, anthu 1 654 330 sadalembetse.

Pachisankho cha 2014, anthu 7 520 816 ndiwo adalembetsa mkaundula kutanthauza kuti odzavota pachisankho cha ulendo uno akuchepera ndi anthu 664 521 kwa omwe adalembetsa kuti akavote mu 2014.

Koma mneneri wa MEC Sangwani Mwafulirwa wanenetsa kuti chiwerengerochi chikhoza kusintha bungwe la MEC likayamba ntchito ya kalondolondo wa kalembera mmalo onse omwe anthu amalembetserako.

“Izi n’zotsatira zomwe zili m’kaundula potengera mapeto a kalembera koma tiyamba ntchito ya kauni. M’kauni, ena amapezeka kuti adalembetsa kawiri pa zolinga zawo ndiye mayina otero timachotsa kumodzi n’kusiya kumodzi choncho anthu asadzadabwe kudzamva kuti ma figala asintha,” watero Mwafulirwa.

Mwa anthu omwe alembetsawa, 3 045 766 ndi abambo pomwe 3 810 625 ndi amayi ndipo Lilongwe ndiyo yalembetsa anthu ambiri 1 013 414 pomwe Likoma ndilo chimtseka khomo ndi anthu 6 946.

Zina mwa zovuta zomwe bungwe la MEC lidakumana nazo mkati mwa kalembera ndi kuonongeka kwa makina opangira kalembera, kuvuta kwa mphamvu ya

magetsi yoyatsira makina ndikunyanyala ntchito kwa ochita kalembera pofuna malipiro makamaka kumayambiriro.

Mabungwe komanso zipani zotsutsa boma zidapereka nkhawa zawo ku bungwe la MEC zokhudza kutsika kwa chiwerengero cha anthu olembetsa ndipo adapempha kuti ngati nkotheka, kalembera akuyenera kudzabwerezedwa m’madera ena omwe zidanyanya.

“Zotsatira za kalembera sizikukhala zabwino koma si vuto la anthu chifukwa akupita mmalo molembetsera koma akubwerera. Bungwe la MEC likuyenera kuchitapo kanthu kuti kalembera adzabwerezedwe,” adatero mneneri wa Malawi Congress Party (MCP) Reverend Maurice Munthali.

Mkulu wa bungwe loona za ufulu wa anthu la Centyre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) Timothy Mtambo adati kupanda kupereka mpata wina wa kalembera n’kuphwanya ufulu wa anthu.

Mawu a Mtambo akutanthauza kuti ufulu wodzaponya voti wa anthu 1 654 330 omwe sadalembetse waphwanyidwa ndipo akuyenera kupatsidwa mpata

wolembetsa kuti nawo adzakhale ndi danga loponya voti.

Kalembera wa m’kaundulayu ndi gawo limodzi la zokonzekera chisankho cha 2019 koma bungwe la MEC silidabwere poyera nkunena ngati liganizire pempho lobwereza kalembera kapena ayi potsatira pempho la mabungwe ndi zipani.

Related Articles

Back to top button
Translate »