Nkhani

‘Mafumu adyera’

Listen to this article

Akatswiri pandale komanso mafumu adzudzula zomwe adachita mafumu ena poyenda ndawala ulendo ku Nyumba ya Malamulo komwe amakatsutsa mabilo a zisankho.

Lachitatu sabata yatha mafumuwo motsogozedwa ndi mfumu Ngolongoliwa, Lundu, Kyungu mwa ena adakasiya kalata kunyumbayo.

Akudana ndi 50+1: mafumuwo ku Nyumba ya Malamulo

Iwo adati sakugwirizana ndi mabilowo omwe mwa zina akufuna kuti mtsogoleri wadziko azisankhidwa ndi anthu oposa 50 pa 100 aliyonse.

Mafumu ena monga Kabunduli wa m’boma la Nkhata Bay wati mafumu amene akupanga izi ndi adyera ndipo akungogwiritsidwa ntchito ndi boma.

“Ili ndi dyera, ufumu ausambula,” adatero Kabunduli. “Mafumu timaimira banja, kodi zonena za banja langa ndingamanene kuti dziko lonse likugwirizana nazo?

“M’ndani adawauza kuti Amalawi akukana 50+1? Ife anatifunsa mafumuwo?” Atafunsidwa ngati iye adaitanidwa kukakhala nawo pa zochitikazo, Kabunduli adati.

“Sangandiuze [za chibwanazo]. Zimenezo amatuma mafumu andale, komanso adyera.”

Mphunzitsi wa za ndale wa ku Chancellor College (Chanco), Happy Kayuni, adati iyi si ntchito yomwe mafumu amayenera kugwira ndipo uku ndi kududuka.

“Timawadziwa mafumu kuti amakhudzidwa ndi nkhani za chikhalidwe, komanso chitukuko. Koma tikuona panozi ndi zosiyana,” adatero Kayuni.

“Andale ndiwo akugwiritsira ntchito molakwika mafumuwa. Ukutu ndi kuphwanya chikhulupiriro chomwe anthu ali nacho mwa mafumuwa.”

Malinga ndi Kayuni, ntchito za mafumuwa zasokonekera kaamba koti akulowerera nkhani zosawakhudza.

“Palibe angaike chikhulupiriro mwa mafumuwa potengera ndi zomwe akuchita. Sizikusiyana ndi andale,” adatero.

Pothirirapo ndemanga pa za kusuluka kwa mphamvu zawo, Kabunduli adati iye wakhala akupita ku Mozambique ndi Zambia komwe anthu amamupatsa ulemu monga mfumu zomwe m’dziko muno sizikuchitika.

“Pano tasanduka andale chifukwa nkhani zomwe si zanthu tayamba kulowerera nawo,” iye adatero.

Mafumu ena a m’maboma a Ntcheu, Mwanza, Mangochi, Mzimba ndi Dedza omwe adakana kutchulidwa adati zomwe anachita mafumuzo ndi maganizo awo osati a anthu kapena mafumu onse.

Pa 29 July 2010, dziko lino lidasintha mbendera yake. Mafumu ndiwo adali patsogolo kuthandizira boma lolamula la DPP kuti mbenderayo isinthe.

Koma pa May 28 2012 yemwe adali mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda, adabwezeretsa mbenderayo.

Joseph Chunga, mphunzitsi wina wa ndale wa ku Chanco, adati mafumuwo adachita izi pofuna kunyengerera boma kuti boma liwakweza udindo.

Ngolongoliwa adati sangalankhule pafoni koma pamaso. Pamene Lundu adati ndiwotangwanika ndipo aimbabe akakhala ndi mpata.

Related Articles

Back to top button