Nkhani

A Malawi akufuna 2018 wa ngwiro

Pomwe chaka cha 2018 changoyamba kumene, mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma Lazarus Chakwera ndi akadaulo ena ati boma lisinthe kayendetsedwe ka zinthu kuti chakachi chikhale chokomera Amalawi.

Chakwera yemwe ndi mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP), kadaulo pa zamaphunziro Benedicto Kondowe, kadaulo pa zachuma Dalitso Kubalasa, kadaulo pa zaumoyo George Jobe ndi mtsogoleri wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira Banda aunikira momwe zinthu zikuyenera kuyendera.

Chakwera: Amalawi amayembekeza zambiri

Akuluakuluwa akhala akudzudzula za momwe boma limayendetsera zinthu zina m’chaka chomwe changothachi ndipo poomba mkota wa madandaulo, Chakwera adati boma lidalephera kukwaniritsa malonjezo ake.

“Padali zinthu zambiri zomwe Amalawi amayembekezera potsatira malonjezo omwe boma lidalonjeza koma momwe chaka cha 2017 chimapita kumapeto, padalibe chomwe chidaonekapo,” adatero Chakwera.

Iye adati mwa zina, boma lidalonjeza kusintha nkhani ya kuthimathima kwa magetsi zomwe sizidatheke mpaka pano, kutukula alimi koma mmalo mwake ndiwo adamva kuwawa kwambiri mchakachi, kuthana ndi katangale zomwe sizidatheke komanso kulemekeza malamulo.

Akuluakuluwa amalankhula ndi Tamvani potsatira mawu a pulezidenti Peter Mutharika polandira chaka chatsopano pomwe adati Amalawi ayembekezere chaka chopambana cha zitukuko.

“Mu 2018, titsegulira ntchito yaikulu ya mthirira yomwe idzapindulire mabanja pafupifupi 40, 000, tipitiriza kutsegula mwayi wa ntchito kwa achinyamata, ntchito za mtukula pakhomo ndi ngongole za achinyamata ndi amayi,” adatero Mutharika.

Kudali kugona kuchigayo kudikira magetsi ayake

Iye adatinso boma lipitiliza kutukula ntchito za chuma powonetsetsa kuti chiwongola dzanja chomwe anthu amapeleka akakongola ndalama ku mabanki chatsika kuti anthu ambiri azitha kutenga ngongole.

“Ndikufuna mchaka chimenechi, mlimi, m’phunzitsi, namwino, msilikali ndi apolisi azitha kulowa m’banki nkutulakamo atatenga ngongole kuti adzipezere malo ndikumanga nyumba zawo,” Mutharika adatero.

Iye adati boma lake lili ndi ndondomeko zomwezidzathandize kuti vuto la magetsi lisadzawonekenso mdziko muno likangotha.

Powonjezerapo pa malonjezowa, nduna ya zamalimidwe, mthilira ndi chitukuko cha madzi Joseph Mwanamvekha adati mchaka cha 2018 boma lipezera alimi misika yabwino ya zokolola kuti apukute misozi yawo.

“Chaka chatha sitikadachitira mwina koma kutseka zipata kuti mbeu zisatuluke mpaka tigule chakudya chokwanira koma poti chaka chino chakudya chiliko kale chokwanira, alimi ayembekezere misika yabwino,” adatero Mwanamvekha

Koma chakwera adati, “Bola izi zisakhale zongofuna kupeleka chiyembekezo kwa Amalawi kuti aziti boma litithandiza. Nthawi yopanga ndale zonamiza anthu idatha, pano ndi nthawi yolankhula ndi ntchito.”

Pounikira za momwe chuma chikuyenera kuyendera, Dalitso Kubalasa yemwe ndi kadaulo pa za chuma adati boma likuyenera kumanga mabawuti kuti nthambi zonse za boma zizitsatira malamulo oyendetsera chuma cha boma.

Iye adati mu 2017, nthambi zina za boma zidapezeka ndi mirandu yosapeleka malipoti a kayendetsedwe ka chuma cha boma zomwe ziapangitsa kuti papezeke mavuto ambiri pa kauniuni wa chuma ha bomachi.

“Tidaona mmene malipoti adalili m’chakachi okhudza kauniuni wa chuma cha boma pomwe ndalama za nkhaninkhani sizidaoneke momwe zidagwirira ntchito. Pamenepa pakuyenera kusinthidwa mchakachi,” adatero Kubalasa.

Iye adati ngati izi sizitheka, ndiye kuti Amalawi ayembekezere chaka china chowawa ku mbali ya za chuma ndipo mabala ake adzavuta kupola kaamba koti chaka chotsatiracho ndi chachisankho.

Benedicto Kondowe yemwe ndi mkulu wa mgwirizano wa bungwe oyang’anira za maphunziro adati boma lisakakamire kutsegula sukulu zokha ndi kusintha maphunziro koma kuti liyike mtima kwambiri pa maphunzirowo apamwamba.

Iye adati maphunziro otukula aphunzitsi apite patsogolo, sukulu zikhale ndi aphunzitsi okwanira, zipangizo zophunzilira ndi ndi kuphunzitsizira zizipezeka mokwanira ndipo oyendera sukulu akhale odzipeleka.

“Ndibwino kuti sukulu zikutsegulidwa koma tikuyenera kuwonetsetsa kuti zipangizo zilimo, aphunzitsi ndiwokwanira komanso ophunzitsidwa bwino ndipo pakhale timu ya akadaulo oyendera kuwona kuti maphunzirowo akuyenda bwinodi,” adatero Kondowe.

Kadaulo wa zaumoyo George Jobe wati potukula ntchito za umoyo, boma liyambe kukwaniritsa mlingo wa mgwirizano wa mayiko oyika K15 pa K100 mu bajeti yake yopita ku unduna wa zaumoyo.

Iye wati mpofunikanso kukhwimitsa malamulo olangira anthu opezeka akuzembetsa mankhwala ndi zipangizo za chipatala kuti zipangizo zoterezi zizikhalamo mzipatala nthawi zonse.

“Nkhani yayikulu apa ndi kukhulupilika ndi kukhala ndi ndondomeko zokhwima bwino zotetezera zipangizo za chipatala. Pamenepa pakukhudzidwanso ndi kukhala ndi ogwira ntchito za chipatala okwaira,” adatero Jobe.

Pulezidenti wa alimi Alfred Kapichira Banda adati alimi sakufuna zambiri koma kudzipeleka ku mbali ya boma pa nkhani yotukula alimi makamaka pa nkhani yolimbana nsi mbozi zomwezikuvuta komansomisika.

Related Articles

Back to top button