Mangani womenya wotsatira MCP

Chipani chotsutsa cha MCP chapempha apolisi kuti aponye m’chitokosi Isaac Jomo Osman, kadeti wa DPP amene adasautsa ndi kuvulitsa mnyamata amene adavala malaya a chipani chotsutsacho.

Lachiwiri m’sabatayi, Osman, yemwe adakhalapo wapampando wa masapota a Big Bullets, adajambulidwa akulamula mnyamatayo amene adavala malaya a makaka a MCP kuti ‘avule ndipo asadzayerekeze kuvala makakawo.’ Izi zidachitika ku Limbe mumzinda wa Blantyre.

Zithunzi zake zidafala: Osman

Mneneri wa MCP Maurice Munthali wati chipani chake chionetsetsa kuti Osman amuthire unyolo chifukwa izi sizofunika mu ulamuliro wa zipani zambiri.

“Kodi anthu akhale mwamantha chifukwa DPP ndiyo ikulamula? Tichite mantha chifukwa cha makadeti? Chilungamo chiyende apapa ndipo tikumemeza apolisi kuti agwire ntchito yawo,” adatero Munthali.

Zithunzi zake zidafala: Osman

Titafunsa mneneri wa polisi kuchigawo cha kummwera Ramsey Mushani ngati chithunzi choonetsa Osman akuthambitsa mnyamatayo wovala za MCP adachiona, iye adati: “Ngati Ramsey Mushani chithunzicho ndachiona, koma ngati ofesi sindidachione.”

Iye adati palibe chomwe apolisi angapange pankhaniyo chifukwa “polisi imadikira wina adandaule osati kupanga ziganizo chifukwa cha zomwe taona pa tsamba la mchezo.”

Mneneri wa DPP Grezeldar Jeffrey adati ndi wotangwanika ndi ntchito zaboma kotero ayankhabe.

Share This Post