Chilima saima nawo

Uli dere n’kulinga utayenda naye. Amene akufuna kuti wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Saulos Chilima adzaimire chipanicho pachisankho cha 2019, ati sakutekeseka ndi ganizo lake lofuna kusamuka m’chipani komanso kukana kukapikisa nawo kumsonkhano waukulu.

Lachitatu, Chilima adabwera poyera koyamba chibadwireni mpungwepungwe m’chipani cha DPP kunena kuti iye sakapikisana nawo pa msonkhano waukulu womwe uchitike mwezi uno. Iye adatinso akukonza zotuluka m’chipanicho ngakhale apitirize kugwira ntchito yake ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino.

Chilima: Sindidzapitako

Anthu ena adatchathuka mu DPP ponena kuti sakufuna mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika koma Chilima amene amati ndi wanthete komanso wa masomphenya.

Gululo limati Chilima apita kukapikisana nawo kumsonkhano waukulu wa chipachino zomwe Chilima wakana ndipo wati sadzapitanso kumsonkhanowo.

Iye watinso ali ndi ganizo lotuluka DPP zomwe azichite posakhalitsapa ponena kuti “pali ndondomeko zoti nditsate” kuti “ndifumuke ndi kuima payekha.”

Ngakhale Chilima wachita zosiyana ndi zomwe omukonda amaganiza, anthuwo akuti ali nganganga pa Chilima mpaka adzatenge dziko lino.

Mmodzi mwa iwo ndi Bon Kalindo amene akuti: “Ifetu ganizo lathu ndi loti Chilima atsogolere dziko lino osati atsogolere DPP, ndiye ganizo lathu sikuti lasintha, ndipo yekha wanenanso kuti abwera poyera ndi kunena zomwe achite mtsogolomu.”

Iye adatsutsa ngati Chilima wawagwiritsa chikolopa. “Ayi sitidagwire chikolopa, dziwani kuti mu DPP mwadzadza ndi ambanda, tidalinso ndi mantha kuti mwina atha kukatikhapa kumsonkhanowo,” adatero iye.

Wina ndi Noel Masangwi amene akuti posakhalitsapa gulu lawo lilankhula kwa Amalawi komabe wati samusiya Chilima mpaka atatsogolera dziko lino.

Koma kadaulo pa ndale Mustapha Hussein wati uwu ungakhale mwayi kwa Chilima kuti atsatidwe ndi khwimbi la anthu.

“Apapa ndiye kuti anthu ena asamuka mu DPP kulondola Chilima. Komanso ena ambali yotsutsa amene amamufuna amulonda. Osaiwalanso achinyamata amene akhala akumufuna,” adatero Hussein.

Kodi izi zingagawanitse DPP? Wachiwiri kwa kwa mneneri wa chipanicho Zelia Chakale wati anthu asaganize choncho.

“DPP ndi gulu la anthu ambiri, ndi chipani chokhazikika. Ife sitikutekeseka koma kulemekeza maganizo awo,” adatero Chakale.

Chilima adauza atolankhani kuti posakhalitsapa abwera poyera ndi kulengeza zomwe achite ngati ayambitse chipani chake, kuthandiza zipani zina kapena kuthandizira Mutharika.

Komabe, iye adathokoza Mutharika pomupatsa mwayi wodziwika ku mtundu wa Amalawi ngati wa ndale atasiya ntchito ku kampani ya Airtel.

Chilima adalonjeza Amalawi kuti iye apitiriza kugwira ntchito ndi Mutharika mpaka nthawi yake itatha.

Mwa zina, iye adadzudzula mchitidwe wa ziphuphu, katangale komanso kusankhana mitundu komwe kukuchitika m’boma.

“Tiyeni tikonde dziko lathu kokana ziphuphu,” adatero iye.

 

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.

Powered by