Nkhani

MEC idzudzula UTM

Listen to this article

Bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission(MEC) ladzudzula gulu la United Transformation Movement (UTM) pokhala nawo m’misonkhano ya bungwe loyang’anira mavuto opezeka nthawi ya zisankho la Multiparty Liaison Committee.

Mamembala a bungweli  amachokera m’zipani zomwe zili m’kaundula wa zipani m’dziko muno, azipembedzo  komanso achitetezo mwa ena.

 

Ansah (2ndR) addressing the press on Wednesday

Gulu la UTM silinalembetse ngati chipani m’dziko muno. Pachifukwa ichi, mamembala  a gulu la UTM sali ovomerezedwa kutenga nawo gawo m’misonkhanoyi.

Koma pomwe bungweli lidapanga msonkhano wawo kuholo ya polisi mumzinda wa Mzuzu Lachisanu lapitalo pokonzekera gawo lomaliza la kalembera wa zisankho, ena mwa mamembala a gululi adali nawo pamsonkhanowu.

Polankhulapo, Commissioner Moffat Banda adati zinthuzi zikulakwika chifukwa zipani zokhazo zomwe zili m’kaundula wa zipani ndi zomwe zikuyenera kukhala nawo pamisonkhanoyi.

“Asapupulume, akadadikira kaye kuti gulu lawo lilowe nawo m’kaundula wa zipani. Apa akuphwanya malamulo,” adatero Banda.

Iye adati gululi likufunika kuuzidwa kuti lisadzapange nawonso misonkhanoyi.

Koma gavanala wa UTM m’chigawo chakumpoto, Afiki Mbewe adati gulu la UTM lizipangabe nawo misonkhanoyo chifukwa ndi limodzi mwa otenga nawo gawo pa zisankho za patatu za chaka chamawa.

Iye adati a bungwe la MEC amaitana onse omwe adzatenge nawo gawo pa zisankho.

“Ifeyo kaya tinalembetsa m’kaundula wa zipani kaya sitinalembetse, koma chaka cha mawa tidzakhala nawo pa mabaloti,” adalongosola Mbewe.

Iye adatinso gulu la UTM lili ndi gawo lalikulu pa zisankho zikubwerazi chifukwa lili ndi anthu ambiri omwe akufuna kuima nawo paukhansala komanso ngati aphungu a Nyumba ya Malamulo.

Related Articles

Back to top button