Nkhani

Olembetsa akuchepa

Listen to this article

Boma la Nsanje likupitilirabe kutsogola pa maboma omwe nantindi wa anthu alembetsa pa ntchito ya kalembera wa m’kaundula wachisankho cha chaka cha mawa.

Ndipo poyerekeza ndi chisankho cha 2014, maboma onse, kupatula a Nsanje, Chikwawa ndi Nkhotakota, anthu alembetsa ochepa kwambiri chaka chino.

Ntchito ya kalembera tsopano yalowera kumpoto

Malinga ndi kalata yomwe lidatulutsa bungwe loyendetsa zisankho m’dziko muno la Malawi Electoral Commission(MEC) lachinayi, lidati pakutha pa gawo 7, anthu omwe alembetsa ndi 6.26 milliyoni.

“Chiwerengerochi ndi chotsika ndi 81peresenti poyerekeza ndi anthu 7.74 miliyoni omwe  bungwe la MEC limayembekezera kuti alembetsa pakutha pa gawo 7,” yatero kalatayo yomwe idasainidwa ndi komishona wa MEC Jean Mathanga.

Chiwerengerochinso ndi chotsika ndi 91 peresenti poyerekeza ndi anthu omwe adalembetsa panthawi yomweyi mchaka cha 2014. Pa nthawiyi, anthu 6.85 miliyoni ndiwo adalembetsa.

Komatu ngakhale ntchitoyu ili kumapeto pomwe gawo lomaliza layamba lero m’maboma a Mzimba, Likoma, Nkhata Bay ndi mzinda wa Mzuzu, zikuoneka kuti Amalawi ambiri sakutenga nawo gawo m’kalemberayu poyerekeza ndi zisankho za m’chaka cha 2014 ndi 2009.

Izitu zikuonetseratu kuti chiwerengerochi chikhonza kudzatsikanso pa nthawi yamavoti tikaunika mbiri ya kavotedwe mdziko muno.

Malinga ndi mneneri wa bungwe la Malawi Electoral Support Network (Mesn) Michael Kachaso, vuto lalikulu lagona poti mabungwe ambiri sadatenge nawo gawo pokaphunzitsa anthu zakufunika kwa kulembetsa.

Iye adati ngakhale bungwe la MEC lidavomereza mabungwe ambiri kukaphunzitsa anthu zokalembetsa, ambiri mwa mabungwewa sadagwire ntchitoyi chifukwa chosowa ndalama.

Kachaso adaonjezeranso kuti Amalawi ambiri sadalembetsenso chifukwa adanyanyala.

“Anthu olembetsa ndiochepa pa zifukwa zambiri monga kunyanyala chifukwa atsogoleri awo sadakwaniritse zomwe adalonjeza,” adalongosola Kachaso.

Iye adaonjezeranso kuti ena sakuona phindu lolembetsa chifukwa ali kale ndi chiphaso cha u nzika.

Apa adati mmbuyomu ena amalembetsa kuti apeze ziphatsozi ndipo pano sakuonanso phindu la kalemberayu.

Kachaso adatinso ngati bungwe la MEC lingaganize zobwerezanso kalemberayu, a mabungwe adzatengepo gawo lalikulu pophunzitsa anthu makamaka omwe alembetsawo kuti adzavote.

Polankhulapo, mkulu wa bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) Ollen Mwalubunju adati bungwe lake layesetsa kumemeza anthu kuti akalembetse m’kaundulayu.

Mwalubunju adati vuto lagona poti anthu ambiri adanyanyala chifukwa atsogoleri omwe adasankha mmbuyomu sadakwaniritse zomwe adalonjeza.

“Ife tikuyesetsa kumbali yathu kuwamema anthu kuti akalembetse ngati akufuna kusintha zinthu chifukwa akangokhumudwa n’kukhazikika, ndi njira imodzi yoti anthu omwe sakuwafuna akhalebe m’mipando,” adalongosola Mwalubunju.

Iye adaonjezeranso kuti malinga ndi malipoti omwe bungwe lake likulandira kuchokera kwa anthu omwe akugwira nawo ntchito m’midzi, Amalawi ambiri akhumudwanso kaamba ka kukula kwa katangale mbali zonse za dziko lino.

“Talephera kuika ndondomeko zotsimikizika zothana ndi vutoli. Anthu ndi okhumudwa kwambiri ndi izi mwa zina, pachifukwa ichi adindo ndi atsogoleri a zipani aunikenso bwino malonjezano awo,” Mwalubunju adatero.

Iye adatinso bungwe la MEC lipange kafukufuku wofufuza zomwe zachititsa kuti anthu ambiri asatuluke.

M’chaka cha 2014 anthu 7.5 miliyoni adalembetsa m’kaundula ngakhale okavota adali 5.2 miliyoni. Izi zikutanthauza kuti pafupifupi 30 peresenti ya anthu olembetsa sidakavote nawo.

Ndipo pamasankho a 2009, anthu pafupifupi 5.8 miliyoni ndiwo adalembetsa pomwe 4.6  miliyoni ndi amene adavota. Apa anthu pafupifupi 22 peresenti sadakavote nawo pamasankhowa.

Kalemberayu adayamba mwezi wa June ndipo akuyembekezereka kutha pa November 9 m’maboma a Mzimba, Nkhata Bay, Likoma ndi mzinda wa Mzuzu. Ntchitoyi yayamba lero.

Related Articles

Back to top button