Mtsutso pa kupikisana nawo kwa olowa zipani
Pamene zipani zina zalengeza zochititsa misonkhano yake yaikulu, pali mtsutso pakati pa akadaulo a ndale pamene zipanizo zikunena kuti sizikufuna ‘alendo’ kuti akapikisane nawo m’mipando yaikulu.
Utsi wafuka kale pa mphala ya ndale pomwe zipani ziwiri cha Malawi Congress Party (MCP) ndi United Democratic Front (UDF) zakhazikitsa mwezi wa August kuti zipite ku kovenshoni.
Komatu zipanizo zanenetsa kuti alendo onse alibe mpata wopikisana nawo pamipando yonona monga wa pulezidenti, wachiwiri wake, mlembi wamkulu ndi wachiwiri wake, msungichuma ndi wachiwiri wake komanso mipando ya komiti yaikulu.
Ngakhale kadaulo pa ndale a Wonderful Mkhutche adati ganizolo ndi labwino kutsogolo la chipani, a George Phiri omwenso ndi kadaulo pa ndale ati kuti demokalase imafunika kupereka kusungitsa bata m’zipani zawo chifukwa mchitidwe wa ziwawa umaononga mbiri ya chipani.
“Nkhani yaikulu ndi kumvetsetsa tanthauzo la ndale ndipo atsogoleri ndiwo ali n’kuthekera kodziwitsa anthu awo kuti kodi ndale ndichiyani ndipo akuyenera kupanga ndale za mtundu wanji,” adatero a Patel.
Mneneri wa mgwirizano wa mabungwe omwe amathandizira kuti zisankho ziziyenda bwino la Malawi Electoral Support Network (Mesn) a MacBain Mkandawire adati ndale zaphindu ndi zotsogoza mfundo.
“Kumenyana kapena kudulirana malire sikutanthauza kuti chipani chapeza mavoti koma mfundo. Anthu amapita kumsonkhano kuti akamve mfundo ndiye palibe chifukwa chomenyana kapena kuthamangitsana koma kunthyakula mfundo,” adatero a Mkandawire.
Wachiwiri kwa wapampando wabungwe lolimbikitsa demokalase la Centre for Multiparty Democracy (CMD) a Elias Chakwera adati akuyembekezera ndale za mtendere pomwe chisankho chikuyandikira. n
mpata kwa aliyense.
A Mkhutche adati: “Mipando ikuluikulu imafunikadi anthu omwe akhala m’chipani kwa kanthawi chifukwa amadziwa ngodya zonse. Amenewa ndiwo angagwire chipani molimba.”
Koma a Phiri adati: “N’chofunika kwambiri kutsegula khomo kwa aliyense, anthu akapikisane ndipo nthumwi zisankhe yemwe zakonda malingana ndi mfundo zake chifukwa sunganeneretu kuti ali ndi nzeru zabwino ndani.”
Chidayamba n’chipani cha MCP kulengeza kuti kovenshoni yake idzachitika pa 8 August 2024 pomwe UDF idalengeza sabata yathayi kuti kovenshoni yake idzachitika pa 3 August 2024.
Chipani cha Alliance for Democracy (Aford) chichititsa kale kovenshoni komwe a Enock Chihana adasankhidwa ngati Pulezidenti wachipanicho ndipo yemwe ankapikisana nawo a Frank Mwenefumbo adayambitsa chipani chawo chotchedwa National Democratic Party (NDP).
Zipani zina zikuluzikulu monga UTM ndi People’s Party (PP) sizidalengeze masiku a kovenshoni ngakhale kuti masiku akuchisankho cha 2025 akusunthira kuchitseko ndipo posachedwapa zipani zidzalowa m’nyengo ya kampeni.
Mmbuyomo, kadaulo pa ndale a Ernest Thindwa adaunikira kuti ndi bwino chipani kupanga kovenshoni nthawi yabwino kuti ngati pangakhale kusemphana kulikonse, mamembala akonzeretu kuti adzayende bwino ku kampeni.
“Simungachotsere kuti kovenshoni ikachitika mikangano ikhalapo, kuchita tsoka, ena amatuluka chipani nkusasuka ndiye mukapanga nthawi yabwino, mumakhala ndi nthawi yokwanira yokonza kusemphanako,” adatero a Thindwa.
Padakalipano, zipani ziwiri zatsopano zabadwa kaamba ka kusemphana m’zipani zakale, a Kondwani Nankhumwa omwe amafuna mpando wa upulezidenti ku DPP adayambitsa chipani cha People’s Democratic Party (PDP).
Nawo a Mwenefumbo adachoka m’chipani cha Aford momwe akhala akulimbirana upulezidenti ndi a Chihana ndipo pano ali m’chipani chawo cha NDP ndipo kumeneko adatsatidwa ndi akuluakulu ena omwe adali ndi maudindo ku Aford monga a Wakuda Kamanga.
Kutengera chiunikiro cha a Thindwa, mamembala enieni a zipani adzaoneka misonkhano ya kovenshoni ikadzachitika kuti adzatsale ndani ndipo adzayalule ndani ndipo adzalowera kuti akadzayalula.