Nkhani

Zipolowe za ndale zikuyala

Listen to this article

Magulu osiyanasiyana kuphatikizapo zipani za ndale ati apolisi asaonerere zipolowe zokhudza ndale zomwe zikuchitika m’dziko muno pounikira kuti zoterezi zimatha kukula.

Maguluwo ati nyengo ino pomwe dziko la Malawi likuthamangitsana ndi nthawi ya chisankho cha patatu cha 2025, atsogoleri a zipani akuyenera kuonetsetsa kuti zipani zawo zikupanga ndale za bata.

A Patel: Atsogoleri asungitse bata

Lachisanu lapitalo pa 17 May 2025 pomwe chipani cha Alliance for Democracy (Aford) chinkakonzekera msonkhano wake pabwalo lamasewero la Mponela, mamembala ake 6 adamenyedwa ndi anthu ena.

Malingana ndi apolisi, anthu omwe adachita chipongwewo sakudziwika ndipo ati iwo akufufuzabe koma kafukufuku wawo akuvutirapo kaamba koti anthu omwe adavulazidwawo sadabwererenso kupolisi atachoka kuchipatala.

“N’zoona lipoti limenelo tili nalo ndipo tili mkati mofufuza koma vuto ndi loti odandaulawo sakuoneka kuti adalowera kuti atachoka kolandira thandizo chifukwa tidawapatsa kalata zoti apite kuchipatala koma sadabwererenso,” watero mneneri wapolisi a Peter Kalaya.

Iwo ati anthuwo atafika kupolisi ya Mponela tsikulo adadandaula kuti adali pabwalo la masewero kukonzekera msonkhano Lamulungu lotsatiralo koma kenako adangoona anthu ena akubwera kenako n’kuyamba kuwamenya.

Koma wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Aford a Timothy Mtambo ati chipani chawo n’chosakhutira ndi momwe apolisiwo akuyendetsera nkhaniyo.

Iwo ati apolisi akuyenera kusintha kagwiridwe kawo ka ntchito chifukwa pamwamba amaonetsa ngati zinthu zikutheka pomwe pansi palibe chomwe chikuchitika ndipo adati izi n’zolakwika komanso zosonkhezera ziwawa za ndale.

“Akaka si koyamba apolisi amapereka chithunzithunzi ngati akupanga kanthu koma atangokhala. Zidachitikanso za nmtundu womwewu ku Lilongwe komwe a chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) adamenyedwa, apolisi adalonjeza kuti akufufuza koma mpaka lero palibe yemwe adagwidwa,” adatero a Mtambo.

Mneneri wa chipani cha DPP a Shadreck Namalomba nawo adadzudzula mtopola womwe mamembala a Aford adachitiridwa ndipo adati boma likukhala ngati silikuona zomwe zikuchitika pomwe likuona.

Kadaulo pa ndale a Nandin Patel adati ndi udindo wa atsogoleri a zipani kusungitsa bata m’zipani zawo chifukwa mchitidwe wa ziwawa umaononga mbiri ya chipani.

“Nkhani yaikulu ndi kumvetsetsa tanthauzo la ndale ndipo atsogoleri ndiwo ali n’kuthekera kodziwitsa anthu awo kuti kodi ndale ndichiyani ndipo akuyenera kupanga ndale za mtundu wanji,” adatero a Patel.

Mneneri wa mgwirizano wa mabungwe omwe amathandizira kuti zisankho ziziyenda bwino la Malawi Electoral Support Network (Mesn) a MacBain Mkandawire adati ndale zaphindu ndi zotsogoza mfundo.

“Kumenyana kapena kudulirana malire sikutanthauza kuti chipani chapeza mavoti koma mfundo. Anthu amapita kumsonkhano kuti akamve mfundo ndiye palibe chifukwa chomenyana kapena kuthamangitsana koma kunthyakula mfundo,” adatero a Mkandawire.

Wachiwiri kwa wapampando wabungwe lolimbikitsa demokalase la Centre for Multiparty Democracy (CMD) a Elias Chakwera adati akuyembekezera ndale za mtendere pomwe chisankho chikuyandikira.

Related Articles

Back to top button