Nkhani

Ndidatseketsa mowabisira

Azakhali,

Mutu wanga waima chifukwa ndazunguzika ndi mavuto omwe ndikukumana nawo. Ine ndi mayi wa ana atatu ndipo ndili pa banja.

Amuna ana anandipatsa pathupi ndili Fomu 2. Iwo anali akugwira ntchito nthawi imeneyo.

Atandipatsa pathupi anakanilira kundikwatira koma makolo anga sankafuna kuti ndilowe m’banja ndidakali wachichepere.

Iwo ananena kuti ndikachira ndibwerere ku sukulu. Amuna anga anawauza makolo anga kuti mwana akadzabadwa ndikutha zaka ziwiri adzanditumiza ku sukulu kuti ndikapitirize. Adanenetsa kuti azidzandilipilira ndi kundilimbikitsa. Ine zimenezi ndidakondwera nazo.

Nditabereka mwana uja, ndidawauza kuti ndiyambe kupita ku sukulu ndidapezeka kuti ndine woyembekezeranso. Iwo anali okondwa kwambiri kuti ndatenga chinja.

Ndidawafotokozera kuti ndiyenera kuyamba kulera koma anandiyankha kuti ino ndi nthawi yoti tizibereka ana osati kupita ku sukulu ayi.

Zimenezi zinandiwawa kwambiri. Akuti mkazi otenga kulera samakhala bwino kuchipinda.

Iwo amanena kuti akufuna ine ndibereke ana 5. Akuti kwawo ndi anthu ochepa ndiye akufuna kuti achuluke. Iwo m’banja mwawo alipo awiri. Iwo ndi mchemwali wawo.

Nditabereka mwana wachitatu ndidakatseketsa koma iwo sindinawauze. Anayamba kudikira kuti ndikhala ndi mwana wina koma sizinatheke.

Makolo anga anayamba kundifunsa chifukwa chimene sindimayambanso sukulu. Ndidawafotokozera amuna anga ndipo anati iwo safuna mkazi woti azidzapikisana naye m’nyumba. Akuti iwo ngati amakwanitsa zonse pakhomo ndiye kuti zili bwino.

Ndinawafokozela makolo anga. Iwo zinawanyasa kwambiri. Andifunsa maganiza anga pa za sukulu ndipo ndinawayankha kuti ndikufuna nditabweleranso kusukulu. Amuna anga akukana. Akuti ana azilera ndi ndani ndiponso akufuna ana akwane 5 osati atatu.

Makolo anga anabwera kwathu kudzawafotokozera amuna za ubwino woti ndibwerere ku sukulu. Amuna anga anawayankha kuti iwo sangasinthe maganizo awo. Ati ine ndi mkazi wawo ndiye ndiyenera kupanga zomwe iwo akufuna. Makolowa andikwiyira akuti chisankho chili ndi ine.

Nditani pamenepa azakhari?

Kuno ku Machinga.

Nditani ine Anatchereza?

Blantyre

Amuna anu alibe chikondi. Ndipo samakukondani. Iwo anakutengani kuti mukhale chowapangila ana. Banja si choncho. Akufuna kuti inu bwenzeretse zomwe kwawo sizinatheke? Samatero.

Nthawi yomwe anakupatsani mimba ndi kuvomera kuti mukachira adzakupititsani ku sukulu linali bodza. Amangofuna kuti akukwatireni basi. Inutu nokha yesetsani kuwakakamiza kuti akuloleni kubwerera ku sukulu.

Zimakhala bwino kuti nonse pa banja muzibweretsa ndalama pa khomo. Inu mukaphuzira ndi kumaliza sukulu ndiye kuti pakhomo panu pazakhala pabwino ngakhale kuti iwo amakwanisa zonse. Komanso kuti bizinesi iyende bwino munthu amayenela kukhala ophunzira.

Chomwe akuyiwala ndi chakuti kunja kuno kuli infa. Iwo atafa ndiye kuti adzakusiyani pa mavuto. Zaka zino aliponso amuna okaniza akazi awo kubwerera ku sukulu kapena kugwira ntchito? Zachikale zimenezo.

Makolo anu akukufunirani zabwino.

Ngati atapitilizebe kukukanizani, pitani kwa ankhoswe kuti akhale nawo pansi.

Akundidyera

Anatche,

Pali mtsikana wina amene ndakhala ndi kumufuna banja nthawi yaitali koma iye akuti sandifuna chifukwa ndine wopanda ndalama. Izi anandiuza mmaso muli gwaaaa. Akuti safuna mwamuna wopanda ndalama.

Anatche, ine ndimagwira ntchito ngakhale kuti sindilandira ndalama zambiri koma ine ndingathe kumusamala koposa omwe akuti ndi a ndalamawo. Mtsikanayu amatha kundipempha ndalama komanso mayunitsi. Ine mtsikanayi ndimamukonda kwambiri. Nditani pamenepa?

Chikondi sitikakamiza achimwene, ngati sakukufunani musiyeni. Mkazi ukamamukakamiza banja umakhala kapolo wake chifukwa amatha kupanga zomwe akufuna mosakuganizira.

Banja limafunika aliyense aziikapo chikondi chake. Banja lokhalamo wekha siliyenda. Inu mutayeni ameneyo. Funafunani mkazi wina.

Akazi ofuna banja, a chikondi, okongola ndi ambiri, zitengera inu kudekha kuti mupeze mkazi wabwino. Osapupuluma ayi.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button